Baibulo la pa intaneti

Zotsatsa


Baibulo lonse Chipangano Chakale Chipangano Chatsopano




Nehemiya 6:2 - Buku Lopatulika

anatumiza mau kwa ine Sanibalati ndi Gesemu, kuti, Tiyeni tikomane kumidzi ya ku Chigwa cha Ono; koma analingirira za kundichitira choipa.

Onani mutuwo

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

anatumiza mau kwa ine Sanibalati ndi Gesemu, kuti, Tiyeni tikomane kumidzi ya ku Chigwa cha Ono; koma analingirira za kundichitira choipa.

Onani mutuwo

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Tsono Sanibalati ndi Gesemu adanditumizira mau onena kuti, “Mubwere, tidzakumane pa mudzi wina m'chigwa cha Ono.” Ankafuna kukandichita chiwembu kumeneko.

Onani mutuwo

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Sanibalati ndi Gesemu, ananditumizira uthenga uwu: “Bwerani tidzakumane pa mudzi wina ku chigwa cha Ono.” Koma iwo anakonzekera kuti akandichite chiwembu kumeneko.

Onani mutuwo



Nehemiya 6:2
15 Mawu Ofanana  

Ndipo Yowabu ananena ndi Amasa, Uli bwino mbale wanga? Ndipo Yowabu anagwira ndevu za Amasa ndi dzanja lake lamanja kuti ampsompsone.


Pofikanso Abinere ku Hebroni, Yowabu anampambutsa kupita naye pakati pa chipata kulankhula naye poduka mphepo; namgwaza pomwepo m'mimba, nafa, chifukwa cha mwazi wa Asahele mbale wake.


Ndi ana a Elipaala: Eberi, ndi Misamu, ndi Semedi, amene anamanga Ono, ndi Lodi ndi midzi yake,


Lodi, ndi Ono, chigwa cha amisiri.


Ndi potsatizana naye anakonza ansembe okhala kuchidikha.


Ndipo ndinawatumizira mithenga, ndi kuti, Ndilikuchita ntchito yaikulu, sindingathe kutsika; ndiidulirenji padera ntchito poileka ine, ndi kukutsikirani?


Amanena za bodza munthu yense ndi mnansi wake, amanena ndi mlomo wothyasika, ndi mitima iwiri.


Woipa apangira chiwembu wolungama, namkukutira mano.


Woipa aunguza wolungama, nafuna kumupha.


Ndiponso ndinapenyera mavuto onse ndi ntchito zonse zompindulira bwino, kuti chifukwa cha zimenezi anansi ake achitira munthu nsanje. Ichinso ndi chabe ndi kungosautsa mtima.


Ndipo anauka Ismaele mwana wa Netaniya, ndi anthu khumi okhala naye, namkantha Gedaliya mwana wa Ahikamu mwana wa Safani ndi lupanga, namupha iye, amene mfumu ya ku Babiloni inamuika wolamulira dziko.


Ndipo akudzera monga amadzera anthu, nakhala pansi pamaso pako ngati anthu anga, namva mau ako, koma osawachita; pakuti pakamwa pao anena mwachikondi, koma mtima wao utsata phindu lao.