2 Samueli 3:27 - Buku Lopatulika27 Pofikanso Abinere ku Hebroni, Yowabu anampambutsa kupita naye pakati pa chipata kulankhula naye poduka mphepo; namgwaza pomwepo m'mimba, nafa, chifukwa cha mwazi wa Asahele mbale wake. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 201427 Pofikanso Abinere ku Hebroni, Yowabu anampambutsa kupita naye pakati pa chipata kulankhula naye poduka mphepo; namgwaza pomwepo m'mimba, nafa, chifukwa cha mwazi wa Asahele mbale wake. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa27 Pamene Abinere ankabwerera ku Hebroni, Yowabu adamtengera pambali, pafupi ndi chipata, nakhala ngati afuna kulankhula naye poduka mphepo. Pomwepo Yowabu adabaya Abinere m'mimba, nkuferatu. Yowabu adachita zimenezi chifukwa choti Abinere anali atamuphera mbale wake Asahele. Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero27 Tsono Abineri atabwerera ku Hebroni, Yowabu anamutengera pambali ku chipata, kukhala ngati akufuna kuyankhula naye mwamseri. Ndipo kumeneko pobwezera imfa ya mʼbale wake Asaheli, Yowabu analasa iyeyo mʼmimba, ndipo anafa. Onani mutuwo |
Ndipo Yehova adzambwezera mwazi wake pamutu wake wa iye yekha, popeza iye anawakantha anthu awiri olungama ndi okoma oposa iye mwini, nawapha ndi lupanga, atate wanga Davide osadziwa, ndiwo Abinere mwana wa Nere kazembe wa khamu la nkhondo la Israele, ndi Amasa mwana wa Yetere kazembe wa khamu la nkhondo la Yuda.
Ndiponso udziwa chimene Yowabu mwana wa Zeruya anandichitira, inde chimene anawachitira akazembe awiri aja a magulu a nkhondo a Israele, ndiwo Abinere mwana wa Nere, ndi Amasa mwana wa Yetere, amene aja anawapha, nakhetsa mwazi ngati wa nkhondo masiku a mtendere, napaka mwazi wa nkhondo pa lamba lake la m'chuuno mwake, ndi pa nsapato za pa mapazi ake.