Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Masalimo 37:12 - Buku Lopatulika

12 Woipa apangira chiwembu wolungama, namkukutira mano.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

12 Woipa apangira chiwembu wolungama, namkukutira mano.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

12 Munthu woipa amachitira upo mnzake wabwino, namamtuzulira maso mwachidani.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

12 Oyipa amakonza chiwembu kutsutsana ndi olungama ndipo amawakukutira mano;

Onani mutuwo Koperani




Masalimo 37:12
16 Mawu Ofanana  

Ndipo anasunga chofunda chake chikhale ndi iye kufikira atabwera kwao mbuyake.


Ndipo Hamani, pakuona kuti Mordekai sanamweramire kapena kumgwadira, mtima wake unadzala mkwiyo.


Koma anachiyesa chopepuka kumthira manja Mordekai yekha; pakuti adamfotokozera mtundu wake wa Mordekai; potero Hamani anafuna kuononga Ayuda onse okhala mu ufumu wonse wa Ahasuwero, ndiwo a mtundu wa Mordekai.


Koma zonsezi sindipindula nazo kanthu konse, pokhala ndilikuona Mordekai Myudayo alikukhala kuchipata cha mfumu.


Pakuti ndamva ugogodi wa ambiri, mantha andizinga. Pondipangira chiwembu, anatsimikiza mtima kulanda moyo wanga.


Yehova aombola moyo wa anyamata ake, ndipo sadzawatsutsa kumlandu onse akukhulupirira Iye.


Pakati pa onyodola pamadyerero, anandikukutira mano.


Woipa aunguza wolungama, nafuna kumupha.


Ndipo khamulo linaperekedwa kwa iyo, pamodzi ndi nsembe yopsereza yachikhalire mwa kulakwa kwake, nkugwetsa pansi choonadi, ndi kuchita chifuniro chake, ndipo inakula.


Ndi mphamvu yake idzakhala yaikulu, koma si mphamvu yakeyake ai, nidzaononga modabwitsa, nidzakuzika, ndi kuchita, ndi kuononga amphamvuwo, ndi anthu opatulikawo.


Tsoka iwo akulingirira chinyengo, ndi kukonza choipa pakama pao! Kutacha m'mawa achichita, popeza chikhozeka m'manja mwao.


Ndipo kuyambira pamenepo iye anafunafuna nthawi yabwino yakuti ampereke Iye.


nakhala upo wakuti amgwire Yesu ndi chinyengo, namuphe.


Nati Saulo, Ndidzampatsa iye, kuti amkhalire msampha, ndi kuti dzanja la Afilisti limgwere. Chifukwa chake Saulo ananena ndi Davide, Lero udzakhala mkamwini wanga kachiwiri.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa