Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Masalimo 37:32 - Buku Lopatulika

32 Woipa aunguza wolungama, nafuna kumupha.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

32 Woipa aunguza wolungama, nafuna kumupha.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

32 Munthu woipa amazonda munthu wabwino, amafunafuna kuti amuphe.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

32 Oyipa amabisala kudikira olungama; kufunafuna miyoyo yawoyo;

Onani mutuwo Koperani




Masalimo 37:32
18 Mawu Ofanana  

Ndipo anasunga chofunda chake chikhale ndi iye kufikira atabwera kwao mbuyake.


Nati iye, Kamuoneni komwe ali; ndikatume munthu kumtenga. Ndipo anamuuza kuti, Ali ku Dotani.


Woipa apangira chiwembu wolungama, namkukutira mano.


Kodi adzapulumuka ndi zopanda pake? Gwetsani anthu mumkwiyo, Mulungu.


Usabisalire, woipa iwe, pomanga wolungama; usapasule popuma iyepo.


Koma ine ndinanga mwanawankhosa wofatsa wotengedwa kukaphedwa; ndipo sindinadziwe kuti anandichitira ine chiwembu, kuti, Tiononge mtengo ndi zipatso zake, timdule iye padziko la amoyo, kuti dzina lake lisakumbukikenso.


Koma, Yehova, mudziwa uphungu wao wonse wakundinenera ine kundipha ine; musakhulukire mphulupulu yao, musafafanize tchimo lao pamaso panu; aphunthwitsidwe pamaso panu; muchite nao m'nthawi ya mkwiyo wanu.


Pakuti ndamva kugogodera kwa ambiri, mantha pozungulira ponse. Neneza, ndipo tidzamneneza iye, ati atsamwali anga onse, amene ayang'anira kutsimphina kwanga; kapena adzakopedwa, ndipo ife tidzampambana iye, ndipo tidzambwezera chilango.


Pamenepo anthu awa anati, Sitidzamtola chifukwa chilichonse Daniele amene, tikapanda kumtola ichi pa chilamulo cha Mulungu wake.


namlindira akakole kanthu kotuluka m'kamwa mwake.


Ndipo panali pamene Iye analowa m'nyumba ya mmodzi wa akulu a Afarisi tsiku la Sabata, kukadya, iwo analikumzonda Iye.


Ndipo anamyang'anira, natumiza ozonda, amene anadzionetsera ngati olungama mtima, kuti akamkole pa mau ake, kotero kuti akampereke Iye ku ukulu ndi ulamuliro wa kazembe.


Ndipo alembi ndi Afarisi analikumzonda Iye, ngati adzachiritsa tsiku la Sabata; kuti akapeze chomneneza Iye.


koma chiwembu chao chinadziwika ndi Saulo. Ndipo anadikiranso pazipata usana ndi usiku kuti amuphe;


Ndipo Saulo anayesa kupyoza Davide kumphatikiza kukhoma ndi mkondowo; koma iye anadzilanditsa kuchoka pamaso pa Saulo; ndipo analasa khoma; ndipo Davide anathawa napulumuka usiku uja.


Ndipo Davide anakhala m'chipululu m'ngaka, nakhala m'dziko la mapiri m'chipululu cha Zifi. Ndipo Saulo anamfunafuna masiku onse, koma Mulungu sadampereke m'dzanja lake.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa