Ndipo dzina lake la ulemerero lidalitsike kosatha; ndipo dziko lonse lapansi lidzale nao ulemerero wake. Amen, ndi Amen.
Mika 2:9 - Buku Lopatulika Muwataya akazi a anthu anga kunja kwa nyumba zao zokondweretsa; muchotsa ulemerero wanga kwa ana ao kosatha. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Muwataya akazi a anthu anga kunja kwa nyumba zao zokondweretsa; muchotsa ulemerero wanga kwa ana ao kosatha. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Akazi a anthu anga mumaŵatulutsa m'nyumba zao zokoma. Ndipo ana ao mumaŵalanda madalitso anga kosalekeza. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mumatulutsa akazi a anthu anga mʼnyumba zawo zabwino. Mumalanda ana awo madalitso anga kosatha. |
Ndipo dzina lake la ulemerero lidalitsike kosatha; ndipo dziko lonse lapansi lidzale nao ulemerero wake. Amen, ndi Amen.
Hema wanga waonongeka, zingwe zanga zonse zaduka; ana anga atuluka mwa ine, palibe iwo; palibenso amene adzamanga hema wanga, kapena kutchinga nsalu zanga.
Ndipo ndidzaika ulemerero wanga mwa amitundu; ndi amitundu onse adzaona chiweruzo changa ndachichita, ndi dzanja langa limene ndinawaikira.
munagulitsanso ana a Yuda ndi ana a Yerusalemu kwa ana a Yavani, kuwachotsa kutali kwa malire ao;
ndiwo amene aliralira fumbi lapansi lili pamutu pa wosauka, napotoza njira ya wofatsa; ndipo munthu ndi atate wake amuka kwa namwali yemweyo, kuti aipse dzina langa loyera;
Ndipo akhumbira minda, nailanda; ngakhale nyumba, nazichotsa; asautsa mwamuna ndi nyumba yake, inde munthu ndi cholowa chake.
Pakuti dziko lapansi lidzadzazidwa ndi chidziwitso cha ulemerero wa Yehova, monga madzi amphimba pansi pa nyanja.
Pakuti Ine, ati Yehova, ndidzakhala kwa iye linga lamoto pozungulira pake, ndipo ndidzakhala ulemerero m'kati mwake.
Koma tsoka inu, alembi ndi Afarisi, onyenga! Chifukwa mutsekera anthu Ufumu wa Kumwamba pamaso pao; pakuti inu nokha simulowamo, ndipo muwaletsa amene alikulowa, kuti asalowemo.
amenewo alusira nyumba za akazi amasiye, napemphera monyenga mau ambiri; amenewa adzalandira kulanga koposa.
amene aononga nyumba za akazi amasiye, ndipo monyenga achita mapemphero aatali; amenewo adzalandira kulanga koposa.
Koma ife tonse ndi nkhope yosaphimbika popenyerera monga mwa kalirole ulemerero wa Ambuye, tisandulika m'chithunzithunzi chomwechi kuchokera kuulemerero kunka kuulemerero, monga ngati kuchokera kwa Ambuye Mzimu.
Pakuti Mulungu amene anati, Kuunika kudzawala kutuluka mumdima, ndiye amene anawala m'mitima yathu kutipatsa chiwalitsiro cha chidziwitso cha ulemerero wa Mulungu pankhope pa Yesu Khristu.
Chifukwa chake mbuye wanga mfumu amvere mau a kapolo wake. Ngati ndi Yehova anakuutsirani inu kutsutsana ndi ine, alandire chopereka; koma ngati ndi ana a anthu, atembereredwe pamaso pa Yehova, pakuti anandipirikitsa lero kuti ndisalandireko cholowa cha Yehova, ndi kuti, Muka, utumikire milungu ina.