1 Samueli 26:19 - Buku Lopatulika19 Chifukwa chake mbuye wanga mfumu amvere mau a kapolo wake. Ngati ndi Yehova anakuutsirani inu kutsutsana ndi ine, alandire chopereka; koma ngati ndi ana a anthu, atembereredwe pamaso pa Yehova, pakuti anandipirikitsa lero kuti ndisalandireko cholowa cha Yehova, ndi kuti, Muka, utumikire milungu ina. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 201419 Chifukwa chake mbuye wanga mfumu amvere mau a kapolo wake. Ngati ndi Yehova anakuutsirani inu kutsutsana ndi ine, alandire chopereka; koma ngati ndi ana a anthu, atembereredwe pamaso pa Yehova, pakuti anandipirikitsa lero kuti ndisalandireko cholowa cha Yehova, ndi kuti, Muka, utumikire milungu ina. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa19 Nchifukwa chake tsono, mbuyanga mfumu, mumve mau a ine mtumiki wanu. Ngati ndi Chauta amene wautsa mtima wanu kuti mundiwukire, Chautayo apepesedwe ndi nsembe. Koma ngati ndi anthu, iwowo Chauta aŵatemberere, pakuti tsono andipirikitsa, kuti ndisakhale nao m'dziko la Chauta. Akuti, ‘Pita katumikire milungu ina.’ Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero19 Tsopano mbuye wanga mfumu tamverani mawu a mtumiki wanu. Ngati ndi Yehova wautsa mtima wanu kuti mundiwukire, ndiye alandire chipepeso. Koma ngati ndi anthu amene achita zimene, ndiye Yehova awatemberere popeza andipirikitsa lero kundichotsa mʼdziko la Yehova, namati, ‘Pita kapembedze milungu ina.’ Onani mutuwo |