Mateyu 9:8 - Buku Lopatulika Ndipo m'mene anthu a makamu anachiona, anaopa, nalemekeza Mulungu, wakupatsa anthu mphamvu yotere. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo m'mene anthu a makamu anachiona, anaopa, nalemekeza Mulungu, wakupatsa anthu mphamvu yotere. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Anthu onse aja ataona zimenezi, adachita mantha, ndipo adatamanda Mulungu amene adapatsa anthu mphamvu zotere. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Gulu la anthu litaona izi, linadzazidwa ndi mantha ndipo linalemekeza Mulungu amene anapereka ulamuliro kwa anthu. |
kotero kuti khamulo linazizwa, pakupenya osalankhula nalankhula, opunduka ziwalo nachira, ndi opunduka miyendo nayenda, ndi akhungu napenya, ndipo iwo analemekeza Mulungu wa Israele.
Ndipo Yesu anadza nalankhula nao, nanena, Mphamvu zonse zapatsidwa kwa Ine Kumwamba ndi padziko lapansi.
Chomwecho muwalitse inu kuunika kwanu pamaso pa anthu, kuti pakuona ntchito zanu zabwino, alemekeze Atate wanu wa Kumwamba.
Ndipo ananyamuka iye pomwepo, nasenza mphasa, natuluka pamaso pa iwo onse; kotero kuti anadabwa onse, nalemekeza Mulungu, nanena kuti, Zotere sitinazione ndi kale lonse.
Ndipo anadabwa kwakukulukulu, nanena, Wachita Iye zonse bwino; angakhale ogontha awamvetsa, ndi osalankhula awalankhulitsa.
Ndipo mmodzi wa iwo, pakuona kuti anachiritsidwa, anabwerera m'mbuyo, nalemekeza Mulungu ndi mau aakulu;
Ndipo pomwepo anapenyanso, namtsata Iye, ndi kulemekeza Mulungu: ndipo anthu onse pakuona, anachitira Mulungu mayamiko.
Ndipo abusawo anabwera, nalemekeza ndi kutamanda Mulungu pa zinthu zonse anazimva, naziona, monga kunalankhulidwa kwa iwo.
Ndipo pamene kenturiyo anaona chinachitikacho, analemekeza Mulungu, nanena, Zoonadi munthu uyu anali wolungama.
Ndipo mantha anagwira onsewo: ndipo analemekeza Mulungu, nanena kuti, Mneneri wamkulu wauka mwa ife; ndipo Mulungu wadzacheza ndi anthu ake.
Mwa ichi alemekezedwa Atate wanga, kuti mubale chipatso chambiri; ndipo mudzakhala ophunzira anga.
Ndipo pamene anamva izi, anakhala duu, nalemekeza Mulungu, ndi kunena, Potero Mulungu anapatsa kwa amitundunso kutembenukira mtima kumoyo.
Ndipo pamene anazimva, analemekeza Mulungu; nati kwa iye, Uona, mbale, kuti ambirimbiri mwa Ayuda akhulupirira; ndipo ali nacho changu onsewa, cha pa chilamulo;
Koma m'mene anawaopsanso anawamasula, osapeza kanthu kakuwalanga, chifukwa cha anthu; pakuti onse analemekeza Mulungu chifukwa cha chomwe chidachitika.
popeza kuti mwa kuyesa kwa utumiki umene alemekeza Mulungu pa kugonja kwa chivomerezo chanu ku Uthenga Wabwino wa Khristu, ndi kwa kuolowa manja kwa chigawano chanu kwa iwo ndi kwa onse;
ndipo mayendedwe anu mwa amitundu akhale okoma, kuti, m'mene akamba za inu ngati ochita zoipa, akalemekeze Mulungu pakuona ntchito zanu zabwino, m'tsiku la kuyang'anira.