Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Machitidwe a Atumwi 4:21 - Buku Lopatulika

21 Koma m'mene anawaopsanso anawamasula, osapeza kanthu kakuwalanga, chifukwa cha anthu; pakuti onse analemekeza Mulungu chifukwa cha chomwe chidachitika.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

21 Koma m'mene anawaopsanso anawamasula, osapeza kanthu kakuwalanga, chifukwa cha anthu; pakuti onse analemekeza Mulungu chifukwa cha chomwe chidachitika.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

21 Abwalowo adaŵachenjezanso moopseza koposa kale, naŵamasula. Sadapeze njira yoti nkuŵalangira, popeza kuti anthu onse ankatamanda Mulungu chifukwa cha zimene zidaachitikazo.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

21 Atawonjeza kuwaopseza anawamasula. Sanathe kugwirizana njira yowalangira, chifukwa anthu onse amayamika Mulungu chifukwa cha zimene zinachitika.

Onani mutuwo Koperani




Machitidwe a Atumwi 4:21
18 Mawu Ofanana  

kotero kuti khamulo linazizwa, pakupenya osalankhula nalankhula, opunduka ziwalo nachira, ndi opunduka miyendo nayenda, ndi akhungu napenya, ndipo iwo analemekeza Mulungu wa Israele.


Ndipo pamene anafuna kumgwira, anaopa makamu a anthu, chifukwa anamuyesa mneneri.


Koma ananena iwo, pa nthawi ya chikondwerero iai, kuti pasakhale phokoso la anthu.


Ndipo m'mene chinatulutsidwa chiwandacho, wosalankhulayo analankhula, ndipo makamu a anthu anazizwa, nanena, Kale lonse sichinaoneke chomwecho mwa Israele.


Ndipo m'mene anthu a makamu anachiona, anaopa, nalemekeza Mulungu, wakupatsa anthu mphamvu yotere.


Ndipo pamene Iye anatero, onse aja akutsutsana naye ananyazitsidwa; ndipo anthu onse a m'khamu anakondwera ndi zinthu zonse za ulemererozo zinachitidwa ndi Iye.


Ndipo alembi ndi ansembe aakulu anafunafuna kumgwira ndi manja nthawi yomweyo; ndipo anaopa anthu; pakuti anazindikira kuti ananenera pa iwo fanizo ili.


Ndiponso, tikanena, Uchokera kwa anthu; anthu onse adzatiponya miyala: pakuti akopeka mtima, kuti Yohane ali mneneri.


Ndipo ansembe aakulu ndi alembi anafunafuna maphedwe ake pakuti anaopa anthuwo.


Ndipo chizizwo chinagwira anthu onse ndipo analemekeza Mulungu; nadzazidwa ndi mantha, nanena kuti, Lero taona zodabwitsa.


Komatu tiwaopse asalankhulenso m'dzina ili kwa munthu aliyense, kuti chisabukenso kwa anthu.


Pakuti anali wa zaka zake zoposa makumi anai munthuyo, amene chizindikiro ichi chakumchiritsa chidachitidwa kwa iye.


Koma palibe mmodzi wa otsalawo analimba mtima kuphatikana nao; komatu anthu anawakuzitsa;


Pamenepo anachoka mdindo pamodzi ndi anyamata; anadza nao, koma osawagwiritsa, pakuti anaopa anthu, angaponyedwe miyala.


Ndipo anavomerezana ndi iye; ndipo m'mene adaitana atumwi, anawakwapula nawalamulira asalankhule kutchula dzina la Yesu, ndipo anawamasula.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa