Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Marko 2:12 - Buku Lopatulika

12 Ndipo ananyamuka iye pomwepo, nasenza mphasa, natuluka pamaso pa iwo onse; kotero kuti anadabwa onse, nalemekeza Mulungu, nanena kuti, Zotere sitinazione ndi kale lonse.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

12 Ndipo ananyamuka iye pomwepo, nasenza mphasa, natuluka pamaso pa iwo onse; kotero kuti anadabwa onse, nalemekeza Mulungu, nanena kuti, Zotere sitinaziona ndi kale lonse.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

12 Munthu uja adadzukadi, natenga machira ake aja nkutuluka, onse aja akuwona. Anthu onse aja adazizwa kwambiri, nayamba kutamanda Mulungu nkumanena kuti, “Zoterezi ife sitinaziwone nkale lonse.”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

12 Anayimirira, nanyamula mphasa yake natuluka onse akumuona. Izi zinadabwitsa aliyense ndipo anayamika Mulungu nati, “Sitinaonepo zinthu ngati izi!”

Onani mutuwo Koperani




Marko 2:12
13 Mawu Ofanana  

Ndipo makamu onse a anthu anazizwa, nanena, Uyu si mwana wa Davide kodi?


kotero kuti khamulo linazizwa, pakupenya osalankhula nalankhula, opunduka ziwalo nachira, ndi opunduka miyendo nayenda, ndi akhungu napenya, ndipo iwo analemekeza Mulungu wa Israele.


Ndipo m'mene chinatulutsidwa chiwandacho, wosalankhulayo analankhula, ndipo makamu a anthu anazizwa, nanena, Kale lonse sichinaoneke chomwecho mwa Israele.


Ndipo m'mene anthu a makamu anachiona, anaopa, nalemekeza Mulungu, wakupatsa anthu mphamvu yotere.


Ndipo anazizwa onse, kotero kuti anafunsana mwa iwo okha, kuti, Ichi nchiyani? Chiphunzitso chatsopano! Ndi mphamvu alamula ingakhale mizimu yonyansa, ndipo imvera Iye.


Ndikuuza iwe, Nyamuka, senza mphasa yako, numuke kwanu.


Ndipo anaika manja ake pa iye; ndipo pomwepo anaongoledwa, nalemekeza Mulungu.


Ndipo mmodzi wa iwo, pakuona kuti anachiritsidwa, anabwerera m'mbuyo, nalemekeza Mulungu ndi mau aakulu;


Ndipo chizizwo chinagwira anthu onse ndipo analemekeza Mulungu; nadzazidwa ndi mantha, nanena kuti, Lero taona zodabwitsa.


Ndipo mantha anagwira onsewo: ndipo analemekeza Mulungu, nanena kuti, Mneneri wamkulu wauka mwa ife; ndipo Mulungu wadzacheza ndi anthu ake.


Koma ambiri a m'khamu la anthu anakhulupirira Iye; ndipo ananena, Pamene Khristu akadza kodi adzachita zizindikiro zambiri zoposa zimene adazichita ameneyo?


Kuyambira pachiyambi sikunamveke kuti wina anatsegulira maso munthu wosaona chibadwire.


Koma m'mene anawaopsanso anawamasula, osapeza kanthu kakuwalanga, chifukwa cha anthu; pakuti onse analemekeza Mulungu chifukwa cha chomwe chidachitika.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa