Ndipo mverani pembedzero la kapolo wanu ndi la anthu anu Aisraele, pamene adzapemphera molunjika kumalo kuno; ndipo mverani Inu mu Mwamba mokhala Inumo; ndipo pamene mukumva, khululukirani.
Mateyu 6:12 - Buku Lopatulika Ndipo mutikhululukire mangawa athu, monga ifenso takhululukira amangawa anthu. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo mutikhululukire mangawa athu, monga ifenso takhululukira amangawa anthu. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Mutikhululukire ife machimo athu, monga ifenso takhululukira otilakwira. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mutikhululukire mangawa athu, monga ifenso tawakhululukira amangawa athu. |
Ndipo mverani pembedzero la kapolo wanu ndi la anthu anu Aisraele, pamene adzapemphera molunjika kumalo kuno; ndipo mverani Inu mu Mwamba mokhala Inumo; ndipo pamene mukumva, khululukirani.
pamenepo mverani Inu mu Mwambamo, ndi kukhululukira tchimo la anthu anu Aisraele, ndi kuwabwezera ku dziko limene munapatsa makolo ao.
pamenepo mverani Inu mu Mwamba mokhala Inu, ndi kukhululukira, ndi kuchita, ndi kubwezera munthu yense monga njira zake zonse, amene Inu mumdziwa mtima wake, popeza Inu, Inu nokha, mudziwa mitima ya ana onse a anthu;
ndi kukhululukira anthu anu adachimwira Inu ndi mphulupulu zao zonse adapalamula nazo kwa Inu; ndipo muwachititsire chifundo iwo amene anawagwira ndende, kuti awachitire chifundo;
wakusungira anthu osawerengeka chifundo, wakukhululukira mphulupulu ndi kulakwa ndi kuchimwa; koma wosamasula wopalamula; wakulanga ana ndi zidzukulu chifukwa cha mphulupulu ya atate ao, kufikira mbadwo wachitatu ndi wachinai.
Tiyeni, tsono, tiweruzane, ati Yehova; ngakhale zoipa zanu zili zofiira, zidzayera ngati matalala; ngakhale zili zofiira ngati kapezi, zidzakhala ngati ubweya wa nkhosa, woti mbuu.
Ambuye, imvani; Ambuye khululukirani; Ambuye, mverani nimuchite; musachedwa, chifukwa cha inu nokha, Mulungu wanga; pakuti mzinda wanu ndi anthu anu anatchedwa dzina lanu.
pakuti ichi ndi mwazi wanga wa pangano wothiridwa chifukwa cha anthu ambiri ku kuchotsa machimo.
Ndipo onani, anabwera naye kwa Iye munthu wamanjenje, wakugona pamphasa: ndipo Yesu pakuona chikhulupiriro chao, anati kwa wodwalayo, Limba mtima, mwana, machimo ako akhululukidwa.
Ndipo pamene muimirira ndi kupemphera, khululukirani, ngati munthu wakulakwirani kanthu; kuti Atate wanunso ali Kumwamba akhululukire inu zolakwa zanu.
Ndipo mutikhululukire ife machimo athu; pakuti ifenso tikhululukira munthu yense wa mangawa athu. Ndipo musatitengere ife kokatiyesa.
Kapena iwo aja khumi ndi asanu ndi atatu, amene nsanja yaitali ya mu Siloamu inawagwera, ndi kuwapha; kodi muyesa kuti iwo anali olakwa koposa anthu onse akukhala m'Yerusalemu?
Potero padziwike ndi inu amuna abale, kuti mwa Iye chilalikidwa kwa inu chikhululukiro cha machimo;
Tili ndi maomboledwe mwa mwazi wake, chikhululukiro cha zochimwa, monga mwa kulemera kwa chisomo chake,
Koma mukhalirane okoma wina ndi mnzake, a mtima wachifundo, akukhululukirana nokha, monganso Mulungu mwa Khristu anakhululukira inu.
kulolerana wina ndi mnzake, ndi kukhululukirana eni okha, ngati wina ali nacho chifukwa pa mnzake; monganso Ambuye anakhululukira inu, teroni inunso;