Eksodo 34:7 - Buku Lopatulika7 wakusungira anthu osawerengeka chifundo, wakukhululukira mphulupulu ndi kulakwa ndi kuchimwa; koma wosamasula wopalamula; wakulanga ana ndi zidzukulu chifukwa cha mphulupulu ya atate ao, kufikira mbadwo wachitatu ndi wachinai. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 20147 wakusungira anthu osawerengeka chifundo, wakukhululukira mphulupulu ndi kulakwa ndi kuchimwa; koma wosamasula wopalamula; wakulangira ana ndi zidzukulu chifukwa cha mphulupulu ya atate ao, kufikira mbadwo wachitatu ndi wachinai. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa7 Amaonetsa chikondi chake kwa anthu zikwi zambirimbiri, ndipo amaŵakhululukira mphulupulu zao, zoipa zao, ndi machimo ao. Koma sadzalekerera ochimwa, ndipo adzalanga ana ndi zidzukulu chifukwa cha zoipa za atate ao, mpaka mbadwo wachitatu ndi wachinai.” Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero7 waonetsa chikondi chosasinthika kwa anthu miyandamiyanda, wokhululukira zoyipa, kuwukira, ndiponso tchimo, komatu salekerera ochimwa kuti asalangidwe. Iye amalanga ana ndi zidzukulu chifukwa cha machimo a makolo awo mpaka mʼbado wachitatu ndi wachinayi.” Onani mutuwo |
Ndipo tsono, Mulungu wathu, ndinu Mulungu wamkulu, ndi wamphamvu, ndi woopsa, wakusunga pangano ndi chifundo, asachepe pamaso panu mavuto athu onse amene anatigwera ife, ndi mafumu athu, akulu athu, ndi ansembe athu, ndi aneneri athu, ndi makolo athu, ndi anthu anu onse, kuyambira masiku a mafumu a Asiriya, mpaka lero lino.