Masalimo 9:4 - Buku Lopatulika Pakuti mwandiweruzira mlandu wanga; mwakhala pa mpando wachifumu, woweruza wolungama. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Pakuti mwandiweruzira mlandu wanga; mwakhala pa mpando wachifumu, woweruza wolungama. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Inu mwatsimikiza kusalakwa kwanga. Mwakhala pa mpando woweruza, mwagamula kuti ndine wosapalamula. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Pakuti Inu mwatsimikiza za kulungama kwanga ndi mlandu wanga; Inu mwakhala pa mpando wanu waufumu, kuweruza mwachilungamo. |
Yehova ndiye gawo la cholowa changa ndi chikho changa, ndinu wondigwirira cholandira changa.
Chilungamo ndi chiweruzo ndiwo maziko a mpando wanu wachifumu; chifundo ndi choonadi zitsogolera pankhope panu.
Pamaso pa Yehova, pakuti akudza; pakuti akudza kudzaweruza dziko lapansi Adzaweruza dziko lokhalamo anthu ndi chilungamo, ndi mitundu ya anthu ndi choonadi.
Pamaso pa Yehova, popeza akudza kudzaweruza dziko lapansi; adzaweruza dziko lokhalamo anthu ndi chilungamo, ndipo mitundu ya anthu molunjika.
koma ndi chilungamo adzaweruza aumphawi, nadzadzudzulira ofatsa a m'dziko moongoka; ndipo adzamenya dziko lapansi ndi chibonga cha kukamwa kwake, nadzapha oipa ndi mpweya wa milomo yake.
amene pochitidwa chipongwe sanabwezere chipongwe, pakumva zowawa, sanaopse, koma anapereka mlandu kwa Iye woweruza kolungama;