Baibulo la pa intaneti

Zotsatsa


Baibulo lonse Chipangano Chakale Chipangano Chatsopano




Masalimo 85:5 - Buku Lopatulika

Kodi mudzatikwiyira nthawi zonse? Kodi mudzakhala chikwiyire mibadwomibadwo?

Onani mutuwo

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

Kodi mudzatikwiyira nthawi zonse? Kodi mudzakhala chikwiyire mibadwomibadwo?

Onani mutuwo

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Kodi mudzakhalabe mukutikwiyira mpaka muyaya? Kodi mudzapitiriza kukwiya mpaka pa mibadwo yathu yonse?

Onani mutuwo

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Kodi mudzatikwiyira mpaka liti? Kodi mudzapitiriza kukwiya pa mibado yathu yonse?

Onani mutuwo



Masalimo 85:5
12 Mawu Ofanana  

Mwaonetsa anthu anu zowawa, mwatimwetsa vinyo wotinjenjemeretsa.


Mulungu, munatitayiranji chitayire? Mkwiyo wanu ufukiranji pa nkhosa za kubusa kwanu?


Kodi Mulungu waiwala kuchita chifundo? Watsekereza kodi nsoni zokoma zake mumkwiyo?


Yehova, mudzakwiya nthawi zonse kufikira liti? Nidzatentha nsanje yanu ngati moto?


Yehova, Mulungu wa makamu, mudzakwiyira pemphero la anthu anu kufikira liti?


Mudzabisala kosatha kufikira liti, Yehova; ndi kuzaza kwanu kudzatentha ngati moto kufikira liti?


Ndani Mulungu wofanana ndi Inu, wakukhululukira mphulupulu, wakupitirira zolakwa za otsala a cholowa chake? Sasunga mkwiyo wake kunthawi yonse popeza akondwera nacho chifundo.


Koma ine, ndidzadikira Yehova; ndidzalindirira Mulungu wa chipulumutso changa; Mulungu wanga adzandimvera.


Ndipo adzagwa ndi lupanga lakuthwa, nadzagwidwa ndende kunka kumitundu yonse ya anthu; ndipo mapazi a anthu akunja adzapondereza Yerusalemu kufikira kuti nthawi zao za anthu akunja zakwanira.


chifukwa chake Yehova anapsera mtima dziko ili kulitengera temberero lonse lolembedwa m'buku ili.