Pakuti mivi ya Wamphamvuyonse yandilowa, mzimu wanga uwumwa ulembe wake; zoopsa za Mulungu zindindandira nkhondo.
Masalimo 7:13 - Buku Lopatulika Ndipo anamkonzera zida za imfa; mivi yake aipanga ikhale yansakali. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo anamkonzera zida za imfa; mivi yake aipanga ikhale yansakali. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Wakonza zida zake zoopsa, waika mivi yamoto ku uta wake. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mulungu wakonza zida zake zoopsa; Iye wakonzekera mivi yake yoyaka moto. |
Pakuti mivi ya Wamphamvuyonse yandilowa, mzimu wanga uwumwa ulembe wake; zoopsa za Mulungu zindindandira nkhondo.
Pakuti, onani, oipa akoka uta, apiringidza muvi wao pansinga, kuwaponyera mumdima oongoka mtima.
Mivi yanu njakuthwa; mitundu ya anthu igwa pansi pa inu; iwalasa mumtima adani a mfumu.
Wathifula uta wake ngati mdani, waima ndi dzanja lake lamanja ngati mmaliwongo; wapha onse okondweretsa maso; watsanulira ukali wake ngati moto pahema wa mwana wamkazi wa Ziyoni.
Dzuwa ndi mwezi zinaima njera mokhala mwao; pa kuunika kwa mivi yanu popita iyo. Pa kung'anipa kwa nthungo yanu yonyezimira.
Munatulukira chipulumutso cha anthu anu, chipulumutso cha odzozedwa anu; munakantha mutu wa nyumba ya woipa, ndi kufukula maziko kufikira m'khosi.
ndikanola lupanga langa lonyezimira, ndi dzanja langa likagwira chiweruzo; ndidzabwezera chilango ondiukira, ndi kulanga ondida.
Mivi yanga ndiiledzeretsa nao mwazi, ndi lupanga langa lidzalusira nyama; ndi mwazi wa ophedwa ndi ogwidwa, ndi mutu wachitsitsi wa mdani.
popeza anatsanulira mwazi wa oyera mtima, ndi wa aneneri, ndipo mudawapatsa mwazi amwe; ayenera iwo.
ndipo anafuula ndi mau aakulu, ndi kunena, Kufikira liti, Mfumu yoyera ndi yoona, muleka kuweruza ndi kubwezera chilango chifukwa cha mwazi wathu, pa iwo akukhala padziko?