Maliro 2:4 - Buku Lopatulika4 Wathifula uta wake ngati mdani, waima ndi dzanja lake lamanja ngati mmaliwongo; wapha onse okondweretsa maso; watsanulira ukali wake ngati moto pahema wa mwana wamkazi wa Ziyoni. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 20144 Wathifula uta wake ngati mdani, waima ndi dzanja lake lamanja ngati mmaliwongo; wapha onse okondweretsa maso; watsanulira ukali wake ngati moto pa hema wa mwana wamkazi wa Ziyoni. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa4 Adalozetsa mivi yake kwa ife ngati mdani wathu, wasamuladi dzanja ngati mdani. Adapha onse amene tinkaŵayang'ana monyadira, pakati pa anthu a mu mzinda wa Ziyoni. Ukali wake unkachita kuyaka ngati moto. Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero4 Wakokera uta wake pa ife ngati ndife adani; wayimiritsa dzanja lake pa ife ngati ndife adani, ndipo anapha onse amene tinkawayangʼana monyadira. Ukali wake ukuyaka ngati moto pa tenti ya mwana wamkazi wa Ziyoni. Onani mutuwo |
Pakuti atero Yehova wa makamu, Mulungu wa Israele: Monga mkwiyo wanga ndi ukali wanga wathiridwa kwa okhala mu Yerusalemu, momwemo ukali wanga udzathiridwa pa inu, pamene mudzalowa mu Ejipito; ndipo mudzakhala chitukwano, ndi chizizwitso, ndi chitemberero, ndi chitonzo; ndipo simudzaonananso malo ano.