Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Maliro 2:5 - Buku Lopatulika

5 Ambuye wasanduka mdani, wameza Israele; wameza zinyumba zake zonse, wapasula malinga ake; nachulukitsira mwana wamkazi wa Yuda maliro ndi chibumo.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

5 Yehova wasanduka mdani, wameza Israele; wameza zinyumba zake zonse, wapasula malinga ake; nachulukitsira mwana wamkazi wa Yuda maliro ndi chibumo.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

5 Chauta adakhala ngati mdani, adaononga Israele. Adaononga nyumba zonse zachifumu, malinga ao onse adaŵasandutsa mabwinja. Adachulukitsa kulira ndi kudandaula pakati pa anthu a ku Yuda.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

5 Ambuye ali ngati mdani; wawonongeratu Israeli; wawonongeratu nyumba zake zonse zaufumu ndipo wawononga malinga ake. Iye wachulukitsa kubuma ndi kulira kwa mwana wamkazi wa Yuda.

Onani mutuwo Koperani




Maliro 2:5
17 Mawu Ofanana  

natentha nyumba ya Yehova, ndi nyumba ya mfumu, ndi nyumba zonse za mu Yerusalemu; ndi nyumba zonse zazikulu anazitentha ndi moto.


Mubisiranji nkhope yanu, ndi kundiyesa mdani wanu?


Wandiyatsiranso mkwiyo wake, nandiyesera ngati wina wa adani ake.


Munapasula makoma ake onse; munagumula malinga ake.


Onse opita panjirapa amfunkhira, akhala chotonza cha anansi ake.


pamenepo ndidzasautsa Ariyele, ndipo padzakhala maliro ndi kulira; koma iye adzakhala kwa Ine monga Ariyele.


Koma iwo anapandukira ndi kumvetsa chisoni mzimu wake woyera, chifukwa chake Iye anasandulika mdani wao, nawathira nkhondo Iye yekha.


Ndipo Yehova anati kwa ine, Ngakhale Mose ndi Samuele akadaima pamaso panga, koma mtima wanga sukadasamalira anthu awa; muwachotse iwo pamaso panga, atuluke.


Yehova, Mulungu wa Israele atero, Taonani, ndidzabweza zida za nkhondo zimene zili m'manja anu, zimene mumenyana nazo ndi mfumu ya ku Babiloni, ndi Ababiloni akuzinga inu, kunja kwa malinga, ndipo ndidzazisonkhanitsa pakati pa mzinda uwu.


Mabwenzi ako onse anakuiwala iwe; salikukufuna iwe; pakuti ndakulasa ndi bala la mdani, ndi kulanga kwa wankhanza; chifukwa cha mphulupulu yako yaikulu, chifukwa zochimwa zako zinachuluka.


ndipo anatentha nyumba ya Yehova ndi nyumba ya mfumu, ndi nyumba zonse za mu Yerusalemu, ngakhale zinyumba zazikulu zonse, anazitentha ndi moto.


Ambuye wameza nyumba zonse za Yakobo osazichitira chisoni; wagumula malinga a mwana wamkazi wa Yuda mwa ukali wake; wawagwetsera pansi, waipitsa ufumuwo ndi akalonga ake.


Wathifula uta wake ngati mdani, waima ndi dzanja lake lamanja ngati mmaliwongo; wapha onse okondweretsa maso; watsanulira ukali wake ngati moto pahema wa mwana wamkazi wa Ziyoni.


naufunyulula pamaso panga; ndipo unalembedwa m'kati ndi kubwalo; munalembedwa m'mwemo nyimbo za maliro, ndi chisoni, ndi tsoka.


Ndipo Samuele ananena naye, Ndipo undifunsiranji ine, popeza Yehova anakuchokera, nasandulika mdani wako?


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa