Zitapita izo, mau a Yehova anadza kwa Abramu m'masomphenya, kuti, Usaope, Abramu, Ine ndine chikopa chako ndi mphotho yako yaikulukulu.
Masalimo 7:10 - Buku Lopatulika Chikopa changa chili ndi Mulungu, wopulumutsa oongoka mtima. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Chikopa changa chili ndi Mulungu, wopulumutsa oongoka mtima. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Mulungu ndiye chishango changa, amapulumutsa anthu olungama mtima. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Chishango changa ndi Mulungu Wammwambamwamba, amene amapulumutsa olungama mtima. |
Zitapita izo, mau a Yehova anadza kwa Abramu m'masomphenya, kuti, Usaope, Abramu, Ine ndine chikopa chako ndi mphotho yako yaikulukulu.
Ndipo iwe Solomoni mwana wanga, umdziwe Mulungu wa atate wako, umtumikire ndi mtima wangwiro ndi moyo waufulu; pakuti Yehova asanthula mitima yonse, nazindikira zolingirira zonse za maganizo; ukamfunafuna Iye udzampeza, koma ukamsiya Iye adzakusiya kosatha.
pamenepo mumvere mu Mwamba mokhala Inumo, nimukhululukire, ndi kubwezera aliyense monga mwa njira zake zonse, monga mudziwa mtima wake; pakuti Inu, Inu nokha, mudziwa mitima ya ana a anthu;
ukakhala woyera ndi woongoka mtima, zoonadi adzakugalamukira tsopano, ndi kupindulitsa pokhala pako polungama.
Ndipo Inu Yehova, ndinu chikopa changa; ulemerero wanga, ndi wondiweramutsa mutu wanga.
Pakuti Yehova Mulungu ndiye dzuwa ndi chikopa; Yehova adzapatsa chifundo ndi ulemerero; sadzakaniza chokoma iwo akuyenda angwiro.
Koma, Yehova wa makamu, amene aweruza molungama, amene ayesa impso ndi mtima, ndikuoneni Inu mulikuwabwezera chilango, pakuti kwa Inu ndawulula mlandu wanga.
Ine Yehova ndisanthula mtima, ndiyesa impso, kuti ndimpatse munthu yense monga mwa njira zake, monga zipatso za ntchito zake.