Momwemo Aisraele onse anakwera nalo likasa la chipangano la Yehova ndi kufuula, ndi kumveka kwa lipenga, ndi mphalasa, ndi nsanje zomveketsa, ndi zisakasa, ndi azeze.
Masalimo 66:1 - Buku Lopatulika Fuulirani kwa Mulungu, dziko lonse lapansi. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Fuulirani kwa Mulungu, dziko lonse lapansi. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Tamandani Mulungu ndi chimwemwe mokweza mau, inu anthu onse a pa dziko lapansi. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Fuwulani kwa Mulungu ndi chimwemwe, dziko lonse lapansi! |
Momwemo Aisraele onse anakwera nalo likasa la chipangano la Yehova ndi kufuula, ndi kumveka kwa lipenga, ndi mphalasa, ndi nsanje zomveketsa, ndi zisakasa, ndi azeze.
Kwa Iye wakuberekeka pamwambamwamba, oyambira kale lomwe; taonani; amveketsa liu lake, ndilo liu lamphamvu.
Fuulirani kwa Yehova, inu, dziko lonse lapansi; kuwitsani ndi kufuulira mokondwera; inde, imbirani zomlemekeza.
Kuchokera ku malekezero a dziko ife tamva nyimbo zolemekeza wolungama. Koma ine ndinati, Ndaonda ine, ndaonda ine, tsoka kwa Ine! Amalonda onyenga amangonyenga; inde ogulitsa onyenga apambana kunyenga.