Yehova, musandichititse manyazi; pakuti ndafuulira kwa Inu, oipa achite manyazi, atonthole m'manda.
Masalimo 4:7 - Buku Lopatulika Mwapatsa chimwemwe mumtima mwanga, chakuposa chao m'nyengo yakuchuluka dzinthu zao ndi vinyo wao. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Mwapatsa chimwemwe mumtima mwanga, chakuposa chao m'nyengo yakuchuluka dzinthu zao ndi vinyo wao. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Koma Inu mwandisangalatsa mtima kwambiri, kupambana anthu a zakudya ndi zakumwa zambiri! Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Inu mwadzaza mtima wanga ndi chimwemwe chachikulu kuposa kuchuluka kwa tirigu wawo ndi vinyo watsopano. |
Yehova, musandichititse manyazi; pakuti ndafuulira kwa Inu, oipa achite manyazi, atonthole m'manda.
Kuti ndipite kufikira guwa la nsembe la Mulungu, kufikira Mulungu wa chimwemwe changa chenicheni, ndi kuti ndikuyamikeni ndi zeze, Mulungu, Mulungu wanga.
Popeza Inu, Yehova, munandikondweretsa ndi kuchita kwanu, ndidzafuula mokondwera pa ntchito ya manja anu.
Undikoke; tikuthamangire; mfumu yandilowetsa m'zipinda zake: Tidzasangalala ndi kukondwera ndi iwe. Tidzatchula chikondi chako koposa vinyo: Akukonda molungama.
Inu mwachulukitsa mtundu, inu mwaenjezera kukondwa kwao; iwo akondwa pamaso panu monga akondwera m'masika, monga anthu akondwa pogawana zofunkha.
Ndipo kusekera ndi kukondwa kwachotsedwa, kumunda wobala ndi kudziko la Mowabu; ndipo ndaletsa vinyo pa zoponderamo; sadzaponda ndi kufuula; kufuula sikudzakhala kufuula.
Koma sanadzisiyire Iye mwini wopanda umboni, popeza anachita zabwino, nakupatsani inu zochokera kumwamba mvula ndi nyengo za zipatso, ndi kudzaza mitima yanu ndi chakudya ndi chikondwero.
amene mungakhale simunamuone mumkonda; amene mungakhale simumpenya tsopano, pokhulupirira, mukondwera naye ndi chimwemwe chosaneneka, ndi cha ulemerero:
Ndipo anatuluka kunka kuminda, natchera mphesa m'mindamo, naponda mphesa, napereka nsembe yolemekeza, nalowa m'nyumba ya mulungu wao, nadya, namwa, natemberera Abimeleki.