Pakukhalabe masiku a dziko lapansi, nthawi yakubzala ndi yakukunkha, chisanu ndi mafundi, malimwe ndi msakasa, usana ndi usiku sizidzalekai.
Masalimo 24:2 - Buku Lopatulika Pakuti Iye analimanga pazinyanja, nalikhazika pamadzi. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Pakuti Iye analimanga pazinyanja, nalikhazika pamadzi. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Pakuti iye ndi amene adaika dziko lapansi pa nyanja yaikulu, adalikhazika pa mitsinje yozama. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero pakuti Iye ndiye anayika maziko ake pa nyanja ndi kulikhazika pamwamba pa madzi. |
Pakukhalabe masiku a dziko lapansi, nthawi yakubzala ndi yakukunkha, chisanu ndi mafundi, malimwe ndi msakasa, usana ndi usiku sizidzalekai.
Zakumwamba zinalengedwa ndi mau a Yehova; ndipo ndi mpweya wa m'kamwa mwake khamu lao lonse.
Yehova achita ufumu; wadziveka ndi ukulu; wadziveka Yehova, wadzimangirira mphamvu m'chuuno; dziko lomwe lokhalamo anthu likhakizika, silidzagwedezeka.
Nenani mwa amitundu, Yehova achita ufumu; dziko lokhalamo anthu lomwe likhazikika kuti silingagwedezeke; adzaweruza mitundu ya anthu molunjika.
Kodi simundiopa Ine? Ati Yehova: simudzanthunthumira pamaso pa Ine, amene ndinaika mchenga chilekaniro cha nyanja, ndi lemba lamuyaya kuti isapitirirepo? Ndipo ngakhale mafunde ake achita gavigavi, alephera; ngakhale akokoma, sangathe kupitirirapo.