Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Masalimo 89:12 - Buku Lopatulika

12 Munalenga kumpoto ndi kumwera; Tabori ndi Heremoni afuula mokondwera m'dzina lanu.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

12 Munalenga kumpoto ndi kumwera; Tabori ndi Heremoni afuula mokondwera m'dzina lanu.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

12 Mudalenga kumpoto ndi kumwera. Mapiri a Tabori ndi Heremoni akukutamandani ndi chimwemwe.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

12 Munalenga Kumpoto ndi Kummwera; Tabori ndi Herimoni akuyimba ndi chimwemwe pa dzina lanu.

Onani mutuwo Koperani




Masalimo 89:12
16 Mawu Ofanana  

Ayala kumpoto popanda kanthu, nalenjeka dziko pachabe.


Kunena za kumwamba, kumwamba ndiko kwa Yehova; koma dziko lapansi analipereka kwa ana a anthu.


Ngati mame a ku Heremoni, akutsikira pa mapiri a Ziyoni. Pakuti pamenepo Yehova analamulira dalitsolo, ndilo moyo womka muyaya.


Dziko lapansi nla Yehova ndi zodzala zake zomwe, dziko lokhalamo anthu ndi iwo okhala m'mwemo.


Pakuti Iye analimanga pazinyanja, nalikhazika pamadzi.


mitsinje iombe m'manja; mapiri afuule pamodzi mokondwera.


Imbani inu, m'mwamba, nukondwere iwe dziko lapansi, imbani inu mapiri, pakuti Yehova watonthoza mtima wa anthu ake, nadzachitira chifundo ovutidwa ake.


Pali Ine, ati Mfumu, dzina lake ndi Yehova wa makamu, ndithu monga Tabori mwa mapiri, monga Karimele pambali pa nyanja, momwemo adzafika.


Ndipo awa ndi mafumu a dzikolo amene ana a Israele anawakantha, nalanda dziko lao tsidya la Yordani kum'mawa, kuyambira chigwa cha Arinoni, mpaka phiri la Heremoni, ndi chidikha chonse cha kum'mawa;


ndi malire anafikira ku Tabori, ndi Sahazuma, ndi Betesemesi; ndi matulukiro a malire ao anali ku Yordani; mizinda khumi ndi isanu ndi umodzi ndi midzi yao.


Ndipo anauza Sisera kuti Baraki mwana wa Abinowamu wakwera kuphiri la Tabori.


Ndipo anatuma, naitana Baraki mwana wa Abinowamu, achoke mu Kedesi-Nafutali; nanena naye, Kodi Yehova Mulungu wa Israele sanalamulire ndi kuti, Muka, nulunjike kuphiri la Tabori, nuwatenge, apite nawe anthu zikwi khumi a ana a Nafutali ndi ana a Zebuloni?


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa