Masalimo 135:5 - Buku Lopatulika Pakuti ndidziwa kuti Yehova ndi wamkulu, ndi Ambuye wathu aposa milungu yonse. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Pakuti ndidziwa kuti Yehova ndi wamkulu, ndi Ambuye wathu aposa milungu yonse. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Pakuti ndimadziŵa kuti Chauta ndi wamkulu, kuti Chauta, Mulungu wathu, ndi wamphamvu kupambana milungu yonse. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Ndikudziwa kuti Yehova ndi wamkulu, kuti Ambuye athu ndi wamkulu kuposa milungu yonse. |
Yehova ndiye wamkulu, ayenera kulemekezekadi, m'mzinda wa Mulungu wathu, m'phiri lake loyera.
Pakuti kuli yani kuthambo timlinganize ndi Yehova? Afanana ndi Yehova ndani mwa ana a amphamvu?
Pakuti Inu, Yehova, ndinu Wam'mwambamwamba padziko lonse lapansi, ndinu wokwezeka kwakukulu pamwamba pa milungu ina yonse.
Ndi Iye amene akhala pamwamba pa malekezero a dziko lapansi, ndipo okhalamo akunga ziwala; amene afutukula thambo ngati chinsalu, naliyala monga hema wakukhalamo;
Chifukwa chake ndilamulira kuti anthu ali onse, mtundu uliwonse, ndi a manenedwe ali onse, akunenera molakwira Mulungu wa Sadrake, Mesaki, ndi Abedenego, adzadulidwa nthulinthuli, ndi nyumba zao zidzasanduka dzala; popeza palibe mulungu wina akhoza kulanditsa motero.
Popeza Yehova Mulungu wanu ndiye Mulungu wa milungu, ndi Mbuye wa ambuye; Mulungu wamkulu, wamphamvu, ndi woopsa, wosasamalira nkhope za anthu, kapena kulandira chokometsera mlandu.