Ndipo akulu a m'nyumba yake ananyamuka, naima pa iye, kuti akamuutse pansi; koma anakana, osafuna kudya nao.
Masalimo 102:4 - Buku Lopatulika Mtima wanga ukunga udzu womweta, nufota; popeza ndiiwala kudya mkate wanga. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Mtima wanga ukunga udzu womweta, nufota; popeza ndiiwala kudya mkate wanga. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Mtima wanga wakanthidwa, ndipo wafota ngati udzu, zoonadi, ngakhale chakudya chimandinyansa. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mtima wanga wakanthidwa ndipo ukufota ngati udzu; ndipo ndimayiwala kudya chakudya changa. |
Ndipo akulu a m'nyumba yake ananyamuka, naima pa iye, kuti akamuutse pansi; koma anakana, osafuna kudya nao.
Pamenepo Ezara ananyamuka pakhomo pa nyumba ya Mulungu, nalowa m'chipinda cha Yehohanani mwana wa Eliyasibu, ndipo atafikako sanadye mkate, sanamwe madzi; pakuti anachita maliro chifukwa cha kulakwa kwa iwo otengedwa ndende.
Mtima wanga ulema nao moyo wanga, ndidzadzilolera kudandaula kwanga, ndidzalankhula pakuwawa mtima wanga.
Pakuti mivi ya Wamphamvuyonse yandilowa, mzimu wanga uwumwa ulembe wake; zoopsa za Mulungu zindindandira nkhondo.
Mulungu wanga, moyo wanga udziweramira m'kati mwanga; chifukwa chake ndikumbukira Inu m'dziko la Yordani, ndi mu Aheremoni, m'kaphiri ka Mizara.
Chotonza chandiswera mtima, ndipo ndidwala ine; ndipo ndinayembekeza wina wondichitira chifundo, koma palibe; ndinayembekeza onditonthoza mtima, osawapeza.