Ndiponso pokhala wanzeru Mlalikiyo anaphunzitsabe anthu nzeru; inde, anatchera makutu nafunafuna nalongosola miyambi yambiri.
Marko 10:1 - Buku Lopatulika Ndipo ananyamuka Iye kumeneko, nadza ku maiko a ku Yudeya ndi ku tsidya lija la Yordani; ndipo anasonkhananso kwa Iye makamu a anthu; ndipo monga anazolowera, anawaphunzitsanso. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo ananyamuka Iye kumeneko, nadza ku maiko a ku Yudeya ndi ku tsidya lija la Yordani; ndipo anasonkhananso kwa Iye makamu a anthu; ndipo monga anazolowera, anawaphunzitsanso. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Yesu adachoka ku Kapernao, napita ku dera la ku Yudeya ndi ku dera la kutsidya kwa mtsinje wa Yordani. Anthu ambirimbiri adadzasonkhananso kwa Iye, ndipo monga ankazoloŵera, adayambanso kuŵaphunzitsa. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Ndipo Yesu anachoka pamalowo ndi kupita kudera la Yudeya ndi kutsidya la mtsinje wa Yorodani. Magulu a anthu anabweranso kwa Iye, ndipo monga mwachizolowezi chake anawaphunzitsa. |
Ndiponso pokhala wanzeru Mlalikiyo anaphunzitsabe anthu nzeru; inde, anatchera makutu nafunafuna nalongosola miyambi yambiri.
Ndipo anandipatsa Ine mbuyo, si nkhope, ngakhale ndinawaphunzitsa, kuuka m'mamawa ndi kuwaphunzitsa, koma sanamvere kulangizidwa.
Nthawi yomweyo Yesu anati kwa makamuwo a anthu, Kodi munatulukira kundigwira Ine ndi malupanga ndi mikunkhu, ngati wachifwamba? Tsiku ndi tsiku ndimakhala mu Kachisi kuphunzitsa, ndipo simunandigwire.
Ndipo Yesu anayendayenda mu Galileya monse, analikuphunzitsa m'masunagoge mwao, nalalikira Uthenga Wabwino wa Ufumu, nachiritsa nthenda zonse ndi kudwala konse mwa anthu.
Ndipo iwo analowa mu Kapernao; ndipo pomwepo pa tsiku la Sabata iye analowa m'sunagoge naphunzitsa.
Ndipo anadza kwa Iye Afarisi, namfunsa Iye ngati kuloledwa kuti munthu achotse mkazi wake, namuyesa Iye.
Ndipo Yesu pamene anaphunzitsa mu Kachisi, anayankha, nanena, Bwanji alembi anena kuti Khristu ndiye mwana wa Davide?
Masiku onse ndinali nanu mu Kachisi ndilikuphunzitsa, ndipo simunandigwire Ine; koma ichi chachitika kuti malembo akwaniritsidwe.
Ndipo anatulukanso kunka m'mbali mwa nyanja; ndipo linadza kwa Iye khamu lonse la anthu, ndipo anawaphunzitsa.
Ndipo pofika tsiku la Sabata, anayamba kuphunzitsa m'sunagoge; ndipo ambiri anamva Iye, nazizwa, nanena, Uyu adazitenga kuti izi? Nzeru yopatsidwa kwa munthuyu njotani, ndi zamphamvu zotere zochitidwa ndi manja ake?
Ndipo anatuluka Iye, naona khamu lalikulu la anthu, nagwidwa chifundo ndi iwo, chifukwa anali ngati nkhosa zopanda mbusa; ndipo anayamba kuwaphunzitsa zinthu zambiri.
Ndipo anazizwa chifukwa cha kusakhulupirira kwao. Ndipo anayendayenda m'midzi yozungulirapo, naphunzitsa.
Ndipo anachoka kunkanso tsidya lija la Yordani, kumalo kumene kunali Yohane analikubatiza poyamba paja; ndipo anakhala komweko.
Yesu anayankha iye, Ine ndalankhula zomveka kwa dziko lapansi; ndinaphunzitsa Ine nthawi zonse m'sunagoge ndi mu Kachisi, kumene amasonkhana Ayuda onse; ndipo mobisika sindinalankhule kanthu.