Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Marko 6:6 - Buku Lopatulika

6 Ndipo anazizwa chifukwa cha kusakhulupirira kwao. Ndipo anayendayenda m'midzi yozungulirapo, naphunzitsa.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

6 Ndipo anazizwa chifukwa cha kusakhulupirira kwao. Ndipo anayendayenda m'midzi yozungulirapo, naphunzitsa.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

6 Ndipo adadabwa poona kuti anthu akumeneko sadamkhulupirire. Pambuyo pake Yesu adapita ku midzi yozungulira, namakaphunzitsa anthu.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

6 Ndipo Iye anadabwa chifukwa chakusowa chikhulupiriro kwawo. Pamenepo Yesu anayenda mudzi ndi mudzi kuphunzitsa.

Onani mutuwo Koperani




Marko 6:6
12 Mawu Ofanana  

Ndipo Iye anaona kuti palibe munthu, nazizwa kuti palibe wopembedzera; chifukwa chake mkono wakewake unadzitengera yekha chipulumutso; ndi chilungamo chake chinamchirikiza.


Kodi mtundu wa anthu unasintha milungu yao, imene siili milungu? Koma anthu anga anasintha ulemerero wao ndi chosapindula.


Ndipo Yesu anayendayenda mu Galileya monse, analikuphunzitsa m'masunagoge mwao, nalalikira Uthenga Wabwino wa Ufumu, nachiritsa nthenda zonse ndi kudwala konse mwa anthu.


Ndipo pakumva ichi, Yesu anazizwa, nati kwa iwo akumtsata, Indetu ndinena kwa inu, ngakhale mwa Israele, sindinapeze chikhulupiriro chotere.


Ndipo Yesu anayendayenda m'mizinda yonse ndi m'midzi, namaphunzitsa m'masunagoge mwao, nalalikira Uthenga Wabwino wa Ufumuwo, nachiritsa nthenda iliyonse ndi zofooka zonse.


Ndipo analowa m'masunagoge mwao mu Galileya monse, nalalikira, natulutsa ziwanda.


Ndipo ananyamuka Iye kumeneko, nadza ku maiko a ku Yudeya ndi ku tsidya lija la Yordani; ndipo anasonkhananso kwa Iye makamu a anthu; ndipo monga anazolowera, anawaphunzitsanso.


Ndipo Iye anapita pakati pa mizinda ndi midzi, naphunzitsa, nayenda ulendo kunkabe ku Yerusalemu.


Ndipo Iye anatsika nadza ku Kapernao, ndiwo mzinda wa ku Galileya. Ndipo analikuwaphunzitsa iwo pa Sabata; ndipo anadabwa ndi chiphunzitso chake;


Ndipo Iye analikulalikira m'masunagoge a ku Yudeya.


Munthuyu anayankha nati kwa iwo, Pakuti chozizwa chili m'menemo, kuti inu simudziwa kumene achokera, ndipo ananditsegulira maso anga.


za Yesu wa ku Nazarete, kuti Mulungu anamdzoza Iye ndi Mzimu Woyera ndi mphamvu; amene anapitapita nachita zabwino, nachiritsa onse osautsidwa ndi mdierekezi, pakuti Mulungu anali pamodzi ndi Iye.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa