Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Mateyu 26:55 - Buku Lopatulika

55 Nthawi yomweyo Yesu anati kwa makamuwo a anthu, Kodi munatulukira kundigwira Ine ndi malupanga ndi mikunkhu, ngati wachifwamba? Tsiku ndi tsiku ndimakhala mu Kachisi kuphunzitsa, ndipo simunandigwire.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

55 Nthawi yomweyo Yesu anati kwa makamuwo a anthu, Kodi munatulukira kundigwira Ine ndi malupanga ndi mikunkhu, ngati wachifwamba? Tsiku ndi tsiku ndimakhala m'Kachisi kuphunzitsa, ndipo simunandigwira.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

55 Pamenepo Yesu adaŵafunsa anthu aja kuti, “Bwanji mwachita kudzandigwira muli ndi malupanga ndi zibonga, ngati kuti ndine chigaŵenga? Tsiku ndi tsiku ndinkakhala pansi m'Nyumba ya Mulungu ndikuphunzitsa, inuyo osandigwira.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

55 Pa nthawi yomweyo Yesu anati kwa gululo, “Kodi ndine mtsogoleri wa anthu owukira kuti mwabwera ndi malupanga ndi zibonga kudzandigwira? Tsiku ndi tsiku ndimakhala mʼNyumba ya Mulungu kuphunzitsa, koma simunandigwire.

Onani mutuwo Koperani




Mateyu 26:55
15 Mawu Ofanana  

Ndipo m'mene Iye analowa mu Kachisi, ansembe aakulu ndi akulu a anthu anadza kwa Iye analikuphunzitsa, nanena, Muchita izi ndi ulamuliro wotani? Ndipo ndani anakupatsani ulamuliro wotere?


Ndipo Iye ali chilankhulire, onani, Yudasi, mmodzi wa khumi ndi awiriwo, anadza, ndi pamodzi ndi iye khamu lalikulu la anthu, ndi malupanga ndi mikunkhu, kuchokera kwa ansembe aakulu ndi akulu a anthu.


Ndipo ananyamuka Iye kumeneko, nadza ku maiko a ku Yudeya ndi ku tsidya lija la Yordani; ndipo anasonkhananso kwa Iye makamu a anthu; ndipo monga anazolowera, anawaphunzitsanso.


Ndipo Yesu pamene anaphunzitsa mu Kachisi, anayankha, nanena, Bwanji alembi anena kuti Khristu ndiye mwana wa Davide?


Ndipo analikuphunzitsa mu Kachisi tsiku ndi tsiku. Koma ansembe aakulu, ndi alembi ndi akulu a anthu anafunafuna kumuononga Iye;


Ndipo kunali lina la masiku ao m'mene Iye analikuphunzitsa anthu mu Kachisi, ndi kulalikira Uthenga Wabwino, adamdzera ansembe aakulu ndi alembi pamodzi ndi akulu;


Ndipo m'mene Iye anapinda bukulo, nalipereka kwa mnyamata, anakhala pansi; ndipo maso ao a anthu onse m'sunagogemo anamyang'anitsa Iye.


Koma pamene padafika pakati pa chikondwerero, Yesu anakwera nalowa mu Kachisi, naphunzitsa.


Pamenepo Yesu anafuula mu Kachisi, alikuphunzitsa ndi kunena, Mundidziwa Ine, ndiponso mudziwa uko ndichokera; ndipo sindinadza Ine ndekha, koma Iye wondituma Ine amene inu simumdziwa, ali woona.


Koma mamawa anadzanso ku Kachisi, ndipo anthu onse anadza kwa Iye; ndipo m'mene anakhala pansi anawaphunzitsa.


Mau awa analankhula m'nyumba yosungiramo chuma cha Mulungu pophunzitsa mu Kachisi; ndipo palibe munthu anamgwira Iye, pakuti nthawi yake siinafike.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa