Mateyu 26:56 - Buku Lopatulika56 Koma izi zonse zinachitidwa, kuti zolembedwa za aneneri zikwaniridwe. Pomwepo ophunzira onse anamsiya Iye, nathawa. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 201456 Koma izi zonse zinachitidwa, kuti zolembedwa za aneneri zikwaniridwe. Pomwepo ophunzira onse anamsiya Iye, nathawa. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa56 Koma zonsezi zachitika kuti ziwonekedi zimene aneneri adalemba.” Pamenepo ophunzira ake onse aja adathaŵa, kumusiya yekha. Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero56 Koma zonsezi zachitika kuti zolembedwa ndi aneneri zikwaniritsidwe.” Pamenepo ophunzira anamusiya nathawa. Onani mutuwo |
Ndipo atapita masabata makumi asanu ndi limodzi mphambu awiri wodzozedwayo adzalikhidwa, nadzakhala wopanda kanthu; ndi anthu a kalonga wakudzayo adzaononga mzinda ndi malo opatulika; ndi kutsiriza kwake kudzakhala kwa chigumula, ndi kufikira chimaliziro kudzakhala nkhondo; chipasuko chalembedweratu.