Mateyu 4:23 - Buku Lopatulika23 Ndipo Yesu anayendayenda mu Galileya monse, analikuphunzitsa m'masunagoge mwao, nalalikira Uthenga Wabwino wa Ufumu, nachiritsa nthenda zonse ndi kudwala konse mwa anthu. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 201423 Ndipo Yesu anayendayenda m'Galileya monse, analikuphunzitsa m'masunagoge mwao, nalalikira Uthenga Wabwino wa Ufumu, nachiritsa nthenda zonse ndi kudwala konse mwa anthu. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa23 Yesu adayendera dziko lonse la Galileya akuphunzitsa m'nyumba zamapemphero ndi kulalika Uthenga Wabwino wonena za ufumu wakumwamba. Ankachiritsanso nthenda zonse za anthu ndi zofooka zao zam'thupi. Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero23 Yesu anayendayenda mu Galileya kuphunzitsa mʼmasunagoge awo, nalalikira Uthenga Wabwino wa ufumu ndi kuchiritsa matenda onse pakati pa anthu. Onani mutuwo |