Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Mateyu 4:22 - Buku Lopatulika

22 Ndipo anasiya pomwepo ngalawayo ndi atate wao, namtsata Iye.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

22 Ndipo anasiya pomwepo ngalawayo ndi atate wao, namtsata Iye.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

22 Pomwepo iwowo adasiya chombo chao ndi bambo wao uja, namatsata Yesu.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

22 Nthawi yomweyo anasiya bwato ndi abambo awo namutsata Iye.

Onani mutuwo Koperani




Mateyu 4:22
10 Mawu Ofanana  

Iye wakukonda atate wake, kapena amake koposa Ine, sayenera Ine, ndipo iye wakukonda mwana wake wamwamuna, kapena wamkazi koposa Ine, sayenera Ine.


Ndipo popitirirapo Iye anaona abale ena awiri, Yakobo mwana wa Zebedeo, ndi Yohane mbale wake, m'ngalawa, pamodzi ndi Zebedeo atate wao, analikusoka makoka ao; ndipo anaitana iwo.


Ndipo Yesu anayendayenda mu Galileya monse, analikuphunzitsa m'masunagoge mwao, nalalikira Uthenga Wabwino wa Ufumu, nachiritsa nthenda zonse ndi kudwala konse mwa anthu.


Ndipo pomwepo anawaitana: ndipo anasiya atate wao Zebedeo m'chombomo pamodzi ndi antchito olembedwa, namtsata.


Munthu akadza kwa Ine, wosada atate wake ndi amake, ndi mkazi wake, ndi ana, ndi abale, ndi alongo ake, inde ndi moyo wake womwe wa iye mwini, sangathe kukhala wophunzira wanga.


Chifukwa chake tsono, yense wa inu amene sakaniza zonse ali nazo, sangathe kukhala wophunzira wanga.


Ndipo m'mene iwo anakocheza ngalawa zao pamtunda, anasiya zonse, namtsata Iye.


Kotero kuti ife sitidziwanso munthu tsopano monga mwa thupi; ndipo ngati tazindikira Khristu monga mwa thupi, koma tsopano sitimzindikiranso motero.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa