Marko 6:2 - Buku Lopatulika2 Ndipo pofika tsiku la Sabata, anayamba kuphunzitsa m'sunagoge; ndipo ambiri anamva Iye, nazizwa, nanena, Uyu adazitenga kuti izi? Nzeru yopatsidwa kwa munthuyu njotani, ndi zamphamvu zotere zochitidwa ndi manja ake? Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 20142 Ndipo pofika tsiku la Sabata, anayamba kuphunzitsa m'sunagoge; ndipo ambiri anamva Iye, nazizwa, nanena, Uyu adazitenga kuti izi? Nzeru yopatsidwa kwa munthuyu njotani, ndi zamphamvu zotere zochitidwa ndi manja ake? Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa2 Litafika tsiku la Sabata, Iye adayamba kuphunzitsa m'nyumba yamapemphero. Anthu ambiri amene ankamvetsera adadabwa kwambiri nkumanena kuti, “Kodi Iyeyu zonsezi adazitenga kuti? Nzeru zimene adalandirazi nzotani? Akutha bwanji kuchita zinthu zamphamvu zotere? Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero2 Tsiku la Sabata litafika, anayamba kuphunzitsa mʼsunagoge, ndipo ambiri amene anamumva anadabwa. Iwo anafunsa kuti, “Kodi munthu uyu anazitenga kuti zimenezi? Kodi ndi nzeru yotani imene munthu ameneyu wapatsidwa, kuti Iye akuchitanso zodabwitsa! Onani mutuwo |