Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Mlaliki 12:9 - Buku Lopatulika

9 Ndiponso pokhala wanzeru Mlalikiyo anaphunzitsabe anthu nzeru; inde, anatchera makutu nafunafuna nalongosola miyambi yambiri.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

9 Ndiponso pokhala wanzeru Mlalikiyo anaphunzitsabe anthu nzeru; inde, anatchera makutu nafunafuna nalongosola miyambi yambiri.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

9 Chifukwa chakuti Mlalikiyo anali waluntha, adaphunzitsa anthu zambiri. Ankasinkhasinkha, kufufuzafufuza ndi kulongosola malangizo mosamala kwambiri.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

9 Mlaliki sanali wozindikira zinthu kokha ayi, komanso ankaphunzitsa anthu. Iye ankasinkhasinkha ndi kufufuzafufuza ndi kulemba mwadongosolo miyambi yambiri.

Onani mutuwo Koperani




Mlaliki 12:9
8 Mawu Ofanana  

Odala anthu anu, odala anyamata anu akukhala nthawi zonse pamaso panu, akumvaimva nzeru yanu.


Ndipo ananena miyambo zikwi zitatu, ndipo nyimbo zake zinali chikwi chimodzi mphambu zisanu.


Ndipo Yehova anapatsa Solomoni nzeru monga momwe adamlonjezera; ndipo panali mtendere pakati pa Hiramu ndi Solomoni, iwo awiri napangana pamodzi.


Miyambo ya Solomoni mwana wa Davide, mfumu ya Israele.


Mwana wanzeru akondweretsa atate; koma mwana wopusa amvetsa amake chisoni.


Iyinso ndiyo miyambo ya Solomoni imene anthu a Hezekiya mfumu ya Yuda anailemba.


Ndipo aphunzitsi adzawala ngati kunyezimira kwa thambo; ndi iwo otembenuza ambiri atsate chilungamo ngati nyenyezi kunthawi za nthawi.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa