Ndipo Abrahamu anamdzudzula Abimeleki chifukwa cha chitsime cha madzi, anyamata ake a Abimeleki anachilanda.
Genesis 26:18 - Buku Lopatulika Ndipo Isaki anafukulanso zitsime za madzi, anazikumba masiku a Abrahamu atate wake; chifukwa kuti Afilisti anazitseka atafa Abrahamu: ndipo anazitcha maina monga maina omwe anazitcha atate wake. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo Isaki anafukulanso zitsime za madzi, anazikumba masiku a Abrahamu atate wake; chifukwa kuti Afilisti anazitseka atafa Abrahamu: ndipo anazitcha maina monga maina omwe anazitcha atate wake. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Kumeneko adafukulanso zitsime zimene anthu adaakumba pa nthaŵi ya Abrahamu bambo wake. Atafa Abrahamuyo, Afilisti adaazikwirira zitsimezo. Isaki adazitcha zitsimezo maina omwewo amene bambo wake ankazitchula. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Isake anafukulanso zitsime zija zimene zinakumbidwa mu nthawi ya abambo ake Abrahamu. Atamwalira Abrahamu, Afilisti anakwirira zitsimezi. Tsono anazitcha mayina omwewo amene abambo ake anazitcha. |
Ndipo Abrahamu anamdzudzula Abimeleki chifukwa cha chitsime cha madzi, anyamata ake a Abimeleki anachilanda.
Ndipo anati, Anaankhosa aakazi asanu ndi awiriwa uwalandire padzanja langa, kuti akhale mboni zanga, kuti ndakumba ine chitsime chimenechi.
Ndipo Isaki anachoka kumeneko, namanga hema wake m'chigwa cha Gerari, nakhala kumeneko.
Ndipo anyamata a Isaki anakumba m'chigwa, napeza kumeneko chitsime cha madzi otumphuka.
Namanga nsanja m'chipululu, nakumba zitsime zambiri; popeza anali nazo zoweta zambiri; kumadambo, ndi kuzidikha; nakhala nao olima minda, ndi osunga mpesa kumapiri ndi kunthaka yopatsa bwino; pakuti anakonda kulima.
Zidzachuluka zisoni zao za iwo otsata Mulungu wina. Sindidzathira nsembe zao zamwazi, ndipo sindidzatchula maina ao pakamwa panga.
Ndipo kudzachitika tsiku lomwelo, ati Yehova wa makamu, ndidzaononga maina a mafano m'dziko; ndipo sadzakumbukikanso; ndipo ndidzachotsa m'dziko aneneri ndi mzimu wachidetso.
ndi Nebo, ndi Baala-Meoni (anasintha maina ao), ndi Sibima; ndipo anaitcha mizinda adaimanga ndi maina ena.