Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




2 Mbiri 26:10 - Buku Lopatulika

10 Namanga nsanja m'chipululu, nakumba zitsime zambiri; popeza anali nazo zoweta zambiri; kumadambo, ndi kuzidikha; nakhala nao olima minda, ndi osunga mpesa kumapiri ndi kunthaka yopatsa bwino; pakuti anakonda kulima.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

10 Namanga nsanja m'chipululu, nakumba zitsime zambiri; popeza anali nazo zoweta zambiri; kumadambo, ndi kuzidikha; nakhala nao olima minda, ndi osunga mpesa kumapiri ndi kunthaka yopatsa bwino; pakuti anakonda kulima.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

10 Pambuyo pake adamanga nsanja ku chipululu ndi kukumba zitsime zambiri, poti anali ndi ziŵeto zambiri ku madambo ndi ku zigwa. Analinso ndi anthu olima minda ndi anthu omasamala mphesa ku mapiri, ndiponso ku maiko achonde, poti ankakonda kulima.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

10 Iye anamanganso nsanja ku chipululu ndi kukumbanso zitsime zambiri chifukwa anali ndi ziweto zambiri mʼmbali mwa phiri ndi ku zigwa. Iye anali ndi anthu amene ankagwira ntchito mʼminda yake ndiponso mʼminda yake ya mphesa mʼphiri ndi malo achonde, pakuti ankakonda nthaka.

Onani mutuwo Koperani




2 Mbiri 26:10
13 Mawu Ofanana  

Watonza Yehova mwa mithenga yako, nuti, Ndi magaleta anga aunyinji ndakwera pa misanje ya mapiri ku mbali zake za Lebanoni, ndipo ndidzagwetsa mikungudza yake yaitali, ndi mitengo yake yosankhika yamlombwa, ndidzalowanso m'ngaka mwake mwenimweni, ku nkhalango zake za madimba.


Ndipo Mesa mfumu ya Mowabu anali mwini nkhosa, akapereka kwa mfumu ya Israele ubweya wa anaankhosa zikwi zana limodzi, ndi wa mphongo zikwi zana limodzi.


Ndipo Yehosafati anakula chikulire, namanga mu Yuda nyumba zansanja, ndi mizinda ya chuma.


Nakhala nazo ntchito zambiri m'mizinda ya Yuda, ndi anthu a nkhondo, ngwazi zamphamvu mu Yerusalemu.


Uziya anali nalonso khamu la anthu a nkhondo, otuluka kunkhondo magulu; nawawerenga monga mwa mawerengedwe ao ndi dzanja la mlembi Yeiyele, ndi kapitao Maaseiya, monga anawauza Hananiya kazembe wina wa mfumu.


Nadzimangiranso mizinda, nadzionera nkhosa ndi ng'ombe zochuluka; pakuti Mulungu adampatsa chuma chambirimbiri.


Ukaona anthu alikutsendereza aumphawi, ndi kuchotsa chilungamo ndi chiweruzo mwachiwawa pa dera lina la dziko, usazizwepo; pakuti mkulu wopambana asamalira; ndipo alipo akulu ena oposa amenewo.


Kodi sikatsala kamphindi kakang'ono, ndipo Lebanoni adzasanduka munda wobalitsa, ndi munda wobalitsa udzayesedwa nkhalango?


mizinda yonse ya kuchidikha, ndi Giliyadi lonse, ndi Basani lonse kufikira ku Saleka ndi Ederei, mizinda ya dziko la Ogi mu Basani.


Maoni, Karimele, ndi Zifi, ndi Yuta;


Ndipo Samuele analawirira m'mawa kuti akakomane ndi Saulo; ndipo munthu anamuuza Samuele kuti, Saulo anafika ku Karimele, ndipo taonani, anaimika chikumbutso chake, nazungulira, napitirira, natsikira ku Giligala.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa