Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Numeri 32:38 - Buku Lopatulika

38 ndi Nebo, ndi Baala-Meoni (anasintha maina ao), ndi Sibima; ndipo anaitcha mizinda adaimanga ndi maina ena.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

38 ndi Nebo, ndi Baala-Meoni (anasintha maina ao), ndi Sibima; ndipo anaitcha midzi adaimanga ndi maina ena.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

38 Nebo, Baala-Meoni (dzina ili lidasinthidwa) ndi Sibima. Mizinda imene adamangayo adaitcha maina ena.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

38 Nebo ndi Baala-Meoni (mayina awa anasinthidwa) ndi Sibima. Anapereka mayina ku mizinda ina yomwe anamangayo.

Onani mutuwo Koperani




Numeri 32:38
15 Mawu Ofanana  

Ndipo Isaki anafukulanso zitsime za madzi, anazikumba masiku a Abrahamu atate wake; chifukwa kuti Afilisti anazitseka atafa Abrahamu: ndipo anazitcha maina monga maina omwe anazitcha atate wake.


A ana a Nebo: Yeiyele, Matitiya, Zabadi, Zebina, Yadai, ndi Yowele, Benaya.


Zidzachuluka zisoni zao za iwo otsata Mulungu wina. Sindidzathira nsembe zao zamwazi, ndipo sindidzatchula maina ao pakamwa panga.


Ndipo samalirani zonse ndanena ndi inu; nimusatchule dzina la milungu ina; lisamveke pakamwa pako.


Pakuti minda ya ku Hesiboni yalefuka, ndi mpesa wa ku Sibima; ambuye a mitundu athyolathyola mitengo yosankhika yake; iwo anafikira ngakhale ku Yazere, nayendayenda m'chipululu; nthambi zake zinatasa, zinapitirira panyanja.


Beli agwada pansi, Nebo awerama; mafano ao ali pa zoweta, ndi pa ng'ombe; zinthu zimene inu munanyamula ponseponse ziyesedwa mtolo, katundu wakulemetsa nyama.


Za Mowabu. Atero Yehova wa makamu, Mulungu wa Israele: Tsoka Nebo! Pakuti wapasuka; Kiriyataimu wachitidwa manyazi, wagwidwa; linga la pamtunda lachitidwa manyazi lapasudwa.


Chiweruzo chafika padziko lachidikha; pa Holoni, ndi pa Yahazi, ndi pa Mefaati;


ndi pa Kiriyataimu, ndi pa Betegamuli, ndi pa Betemeoni;


chifukwa chake taona ndidzatsegula pambali pake pa Mowabu kuyambira kumizinda, kumizinda yake yokhala mphepete, yokometsetsa ya m'dziko, Beteyesimoti, Baala-Meoni, ndi Kiriyataimu,


Ndipo kunali kuti m'mawa, Balaki anatenga Balamu, nakwera naye ku misanje ya Baala, ndi kumeneko anaona malekezero a anthuwo.


Ataroti, ndi Diboni, ndi Yazere, ndi Nimira, ndi Hesiboni, ndi Eleyale, ndi Sibima, ndi Nebo, ndi Beoni,


Ndipo ana a Rubeni anamanga Hesiboni, ndi Eleyale, ndi Kiriyataimu;


nufe m'phiri m'mene ukweramo, nuitanidwe kunka kwa anthu a mtundu wako; monga Aroni mbale wako anafa m'phiri la Hori, naitanidwa kunka kwa anthu a mtundu wake;


osalowa pakati pa amitundu awa otsala mwa inu; kapena kutchula dzina la milungu yao; osalumbiritsa nalo, kapena kuitumikira, kapena kuigwadira;


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa