Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Genesis 21:31 - Buku Lopatulika

31 Chifukwa chake anatcha malowo Beereseba: chifukwa pamenepo analumbira onse awiri.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

31 Chifukwa chake anatcha malowo Beereseba: chifukwa pamenepo analumbira onse awiri.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

31 Motero malo amenewo adatchedwa Beereseba chifukwa kumeneko ndiko kumene anthu aŵiriwo adachita chipangano.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

31 Kotero malo amenewo anatchedwa Beeriseba, chifukwa anthu awiriwo analumbirirapo malumbiro.

Onani mutuwo Koperani




Genesis 21:31
14 Mawu Ofanana  

Ndipo Abrahamu analawira m'mamawa, natenga mkate ndi thumba la madzi, nampatsa Hagara, naika paphewa pake, ndi mwana, namchotsa iye: ndipo iye anamuka, nasocherera m'chipululu cha Beereseba.


Ndipo anapangana pangano pa Beereseba: ndipo anauka Abimeleki ndi Fikolo kazembe wa nkhondo yake, nabwera kunka ku dziko la Afilisti.


Ndipo anachoka kumeneko nakwera kunka ku Beereseba.


Ndipo analawira m'mamawa nalumbirirana wina ndi mnzake; ndipo Isaki anawalola amuke, ndipo anauka kuchokera kwa iye m'mtendere.


Ndipo anatcha dzina lake Siba, chifukwa chake dzina la mzindawo ndi Beereseba kufikira lero lino.


Ndipo Israele anamuka ulendo wake ndi zonse anali nazo, nafika ku Beereseba, napereka nsembe kwa Mulungu wa Isaki atate wake.


Koma uphungu wanga ndiwo kuti musonkhanitse Aisraele onse kwa inu kuyambira ku Dani kufikira ku Beereseba, monga mchenga uli panyanja kuchuluka kwao; ndi kuti mutuluke kunkhondo mwini wake.


nafika ku linga la Tiro ndi kumizinda yonse ya Ahivi ndi ya Akanani; natulukira kumwera kwa Yuda ku Beereseba.


Ndipo iye ataona chimenechi, ananyamuka, nathawa kupulumutsa moyo, nafika ku Beereseba wa ku Yuda, nasiya mnyamata wake pamenepo.


Ndipo Ayuda ndi Aisraele anakhala mosatekeseka, munthu yense patsinde pa mpesa wake ndi mkuyu wake, kuyambira ku Dani mpaka ku Beereseba, masiku onse a Solomoni.


ndi mu Hazara-Suwala, ndi mu Beereseba ndi midzi yake,


koma musamafuna Betele, kapena kumalowa mu Giligala; musamapita ku Beereseba; pakuti Giligala adzalowadi m'ndende, ndi Betele adzasanduka chabe.


ndi Hazara-Suwala, ndi Beereseba, ndi Biziyotiya;


Pamenepo anatuluka ana onse a Israele, nuunjikana msonkhano kwa Yehova ku Mizipa ngati munthu mmodzi, kuyambira ku Dani mpaka Beereseba ndi dziko la Giliyadi lomwe.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa