Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Genesis 21:30 - Buku Lopatulika

30 Ndipo anati, Anaankhosa aakazi asanu ndi awiriwa uwalandire padzanja langa, kuti akhale mboni zanga, kuti ndakumba ine chitsime chimenechi.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

30 Ndipo anati, Anaankhosa akazi asanu ndi awiriwa uwalandire pa dzanja langa, kuti akhale mboni zanga, kuti ndakumba ine chitsime chimenechi.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

30 Abrahamu adayankha kuti, “Inu landirani nkhosa zisanu ndi ziŵirizi, chifukwa mukatero mukuvomereza kuti chitsimechi ndidakumba ndine.”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

30 Iye anayankha kuti, “Landirani ana ankhosa aakazi kuchokera mʼdzanja langa ngati umboni kuti ndinakumba chitsime ichi.”

Onani mutuwo Koperani




Genesis 21:30
8 Mawu Ofanana  

Ndipo Abrahamu anapatula anaankhosa aakazi asanu ndi awiri pa okha.


Ndipo Abimeleki anati kwa Abrahamu, Nanga anaankhosa aakazi asanu ndi awiri amene wapatula pa okha?


Ndipo zitsime zonse anakumba anyamata a atate wake, Abrahamuyo akali moyo, Afilisti anazitseka, nazikwirira ndi dothi.


Ndipo Isaki anafukulanso zitsime za madzi, anazikumba masiku a Abrahamu atate wake; chifukwa kuti Afilisti anazitseka atafa Abrahamu: ndipo anazitcha maina monga maina omwe anazitcha atate wake.


Muluwu ndiwo mboni, choimiritsachi ndicho mboni, kuti ine sindidzapitirira pa muluwu kunka kwa iwe, ndipo iwe sudzapitirira pa muluwu ndi pa choimiritsachi kudza kwa ine kuti tichitirane zoipa.


Ndipo Yoswa anati kwa anthu onse, Taonani, mwala uwu udzakhala mboni yotitsutsa; pakuti udamva mau onse a Yehova amene ananena kwa ife; ndipo udzakhala mboni yotsutsa inu, mungakanize Mulungu wanu.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa