Ndipo Solomoni anaimirira ku guwa la nsembe la Yehova pamaso pa msonkhano wonse wa Israele, natambasulira manja ake kumwamba, nati,
Eksodo 9:29 - Buku Lopatulika Ndipo Mose ananena naye, Potuluka m'mzinda ine, ndidzakweza manja anga kwa Yehova; mabingu adzaleka, ndi matalala sadzakhalaponso; kuti mudziwe kuti dziko lapansi nla Yehova. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo Mose ananena naye, Potuluka m'mudzi ine, ndidzasasatulira manja anga kwa Yehova; mabingu adzaleka, ndi matalala sadzakhalaponso; kuti mudziwe kuti dziko lapansi nla Yehova. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Mose adamuuza kuti, “Ndikangotuluka mumzinda muno, ndikweza manja anga kwa Chauta. Tsono mabingu ndi matalala aleka, kuti inuyo mudziŵe kuti dziko lonse lapansi ndi la Chauta. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mose anayankha, “Ndikangotuluka mu mzinda muno, ine ndidzakweza manja anga kwa Yehova ndi kupemphera. Mabingu ndi matalalawa adzaleka ndipo inu mudzadziwa kuti Yehova ndiye akulamulira dziko lapansi. |
Ndipo Solomoni anaimirira ku guwa la nsembe la Yehova pamaso pa msonkhano wonse wa Israele, natambasulira manja ake kumwamba, nati,
tsono pempho ndi pembedzero lililonse akalipempha munthu aliyense, kapena anthu anu onse Aisraele, pakuzindikira munthu yense chinthenda cha mtima wa iye yekha, ndi kutambasulira manja ake kunyumba ino;
Ndi pa nsembe yamadzulo ndinanyamuka m'kuzunzika kwanga, chovala changa ndi malaya anga zong'ambika; ndipo ndinagwada ndi maondo anga, ndi kutambasula manja anga kwa Yehova Mulungu wanga;
Chilichonse chimkonda Yehova achichita, kumwamba ndi padziko lapansi, m'nyanja ndi mozama monse.
Ndipo tsopano, ngati mudzamvera mau anga ndithu, ndi kusunga chipangano changa, ndidzakuyesani chuma changa cha padera koposa mitundu yonse ya anthu; pakuti dziko lonse lapansi ndi langa;
chifukwa m'masiku asanu ndi limodzi Yehova adalenga kumwamba ndi dziko lapansi ndi nyanja ndi zinthu zonse zili m'menemo, napumula tsiku lachisanu ndi chiwiri; chifukwa chake Yehova anadalitsa tsiku la Sabata kuti likhale lopatulika.
Ndipo tsiku ilo ndidzalemba malire dziko la Goseni, m'mene mukhala anthu anga, kuti pamenepo pasakhale mizaza; kotero kuti udziwe kuti Ine ndine Yehova pakati padzikoli.
Ndipo Aroni anatambasula dzanja lake pamadzi a mu Ejipito; ndipo anakwera achule, nakuta dziko la Ejipito.
Ndipo Mose anatuluka kwa Farao m'mzinda nakweza manja ake kwa Yehova; ndipo mabingu ndi matalala analeka, ndi mvula siinavumbanso padziko.
Ndipo pamene mutambasula manja anu, ndidzakubisirani inu maso anga; inde pochulukitsa mapemphero anu Ine sindidzamva; manja anu adzala mwazi.
Koma ngati wina akati kwa inu, Yoperekedwa nsembe iyi, musadye, chifukwa cha iyeyo wakuuza, ndi chifukwa cha chikumbumtima.
Taonani thambo, ndi kumwambamwamba, dziko lapansi, ndi zonse zili m'mwemo ndi zake za Yehova Mulungu wanu.