Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




1 Akorinto 10:28 - Buku Lopatulika

28 Koma ngati wina akati kwa inu, Yoperekedwa nsembe iyi, musadye, chifukwa cha iyeyo wakuuza, ndi chifukwa cha chikumbumtima.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

28 Koma ngati wina akati kwa inu, Yoperekedwa nsembe iyi, musadye, chifukwa cha iyeyo wakuuza, ndi chifukwa cha chikumbu mtima.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

28 Koma wina akakuuzani kuti, “Nyama iyi idaperekedwa kwa mafano,” apo ndiye musadye nyamayo. Chifukwa cha amene wakuuzayo, usadye nyamayo, kuwopa kuti mtima ungavutike.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

28 Koma ngati wina akuwuzani kuti, “Izi zaperekedwa nsembe,” musadye zimenezo, pofuna kuthandiza amene wakuwuzaniyo komanso chifukwa cha chikumbumtima.

Onani mutuwo Koperani




1 Akorinto 10:28
11 Mawu Ofanana  

Kunena za kumwamba, kumwamba ndiko kwa Yehova; koma dziko lapansi analipereka kwa ana a anthu.


Dziko lapansi nla Yehova ndi zodzala zake zomwe, dziko lokhalamo anthu ndi iwo okhala m'mwemo.


Ndipo Mose ananena naye, Potuluka m'mzinda ine, ndidzakweza manja anga kwa Yehova; mabingu adzaleka, ndi matalala sadzakhalaponso; kuti mudziwe kuti dziko lapansi nla Yehova.


Koma ngati iwe wachititsa mbale wako chisoni ndi chakudya, pamenepo ulibe kuyendayendanso ndi chikondano. Usamuononga ndi chakudya chako, iye amene Khristu adamfera.


pakuti dziko lapansi lili la Ambuye, ndi kudzala kwake.


Komatu chidziwitso sichili mwa onse; koma ena, ozolowera fano kufikira tsopano, adyako monga yoperekedwa nsembe kwa fano; ndipo chikumbumtima chao, popeza nchofooka, chidetsedwa.


Koma yang'anirani kuti ulamuliro wanu umene ungakhale chokhumudwitsa ofookawo.


Taonani thambo, ndi kumwambamwamba, dziko lapansi, ndi zonse zili m'mwemo ndi zake za Yehova Mulungu wanu.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa