pakuti sindinakhale m'nyumba kuyambira tsiku lija ndinakwera naye Israele, kufikira lero lino; koma ndakhala ndikuyenda m'mahema uku ndi uku.
Eksodo 40:2 - Buku Lopatulika Tsiku loyamba la mwezi woyamba ukautse Kachisi wa chihema chokomanako. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Tsiku loyamba la mwezi woyamba ukautse Kachisi wa chihema chokomanako. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa “Pa tsiku loyamba la mwezi woyamba, uutse chihema chamsonkhano. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero “Imika chihema, tenti ya msonkhano, tsiku loyamba la mwezi. |
pakuti sindinakhale m'nyumba kuyambira tsiku lija ndinakwera naye Israele, kufikira lero lino; koma ndakhala ndikuyenda m'mahema uku ndi uku.
Chaka choyamba cha ufumu wake, mwezi woyamba, anatsegula pa makomo a nyumba ya Yehova, napakonzanso.
Mwezi wachitatu atatuluka ana a Israele m'dziko la Ejipito, tsiku lomwelo, analowa m'chipululu cha Sinai.
Ndipo uzipanga chihema ndi nsalu zophimba khumi, za bafuta wa thonje losansitsa, ndi thonje lamadzi, ndi lofiirira, ndi lofiira; uombemo akerubi, ntchito ya mmisiri.
Ndipo uziomba nsalu zophimba za ubweya wa mbuzi zikhale chophimba pamwamba pa chihema; uziomba nsalu khumi ndi imodzi.
Aroni ndi ana ake aikonze m'chihema chokomanako, pamaso pa Yehova, kunja kwa nsalu yotchinga yokhala kumboni, kuyambira madzulo kufikira m'mawa; likhale lemba losatha mwa mibadwo yao, alisunge ana a Israele.
nupere china chisalale, nuchiike chakuno cha mboni m'chihema chokomanako, kumene ndidzakomana ndi iwe; uchiyese chopatulika ndithu.
chihema, ndi chophimba chake, zokowera zake, ndi matabwa ake, mitanda yake, mizati, nsanamira, ndi nsichi zake, ndi makamwa ao;
Ndipo anapanga zokowera makumi asanu zamkuwa kumanga pamodzi hemalo, kuti likhale limodzi.
Ndipo ukaike guwa la nsembe yopsereza kunja kwa khomo la Kachisi wa chihema chokomanako.
Chaka cha makumi awiri ndi zisanu cha undende wathu, poyamba chaka, tsiku lakhumi lamwezi, chaka chakhumi ndi zinai atakantha mzindawo, tsiku lomwelo, dzanja la Yehova linandikhalira; ndipo anamuka nane komweko.
Atero Ambuye Yehova, Mwezi woyamba, tsiku loyamba la mwezi, uzitenga mwanawang'ombe wopanda chilema, ndipo uyeretse malo opatulika.
Ndipo Yehova ananena ndi Mose m'chipululu cha Sinai, m'chihema chokomanako, tsiku loyamba la mwezi wachiwiri, chaka chachiwiri atatuluka m'dziko la Ejipito, ndi kuti,
Ndipo kunali kuti tsiku lomwe Mose anatsiriza kuutsa chihema, nachidzoza ndi kuchipatula, ndi zipangizo zake zonse, ndi guwa la nsembe, ndi zipangizo zake zonse, nazidzoza ndi kuzipatula;
Ndipo Yehova ananena ndi Mose m'chipululu cha Sinai, mwezi woyamba wa chaka chachiwiri atatuluka m'dziko la Ejipito, ndi kuti,
Ndipo tsiku loutsa Kachisi mtambo unaphimba Kachisi, ndiwo chihema chokomanako; ndicho chihema chaumboni, ndipo madzulo padaoneka pa Kachisi ngati moto, kufikira m'mawa.