Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Numeri 9:15 - Buku Lopatulika

15 Ndipo tsiku loutsa Kachisi mtambo unaphimba Kachisi, ndiwo chihema chokomanako; ndicho chihema chaumboni, ndipo madzulo padaoneka pa Kachisi ngati moto, kufikira m'mawa.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

15 Ndipo tsiku loutsa Kachisi mtambo unaphimba Kachisi, ndiwo chihema chokomanako; ndicho chihema chaumboni, ndipo madzulo padaoneka pa Kachisi ngati moto, kufikira m'mawa.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

15 Pa tsiku limene adamanga malo opatulika, mtambo udaphimba malo opatulikawo, ndiye kuti chihema chaumboni chija. Madzulo aliwonse mpaka m'maŵa mwake, mtambowo unkaphimba malo opatulika uli ndi maonekedwe a moto.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

15 Pa tsiku limene anayimika chihema, tenti ya umboni, mtambo unaphimba chihemacho. Kuyambira madzulo mpaka mmawa, mtambo umene unali pamwamba pa chihemacho unkaoneka ngati moto.

Onani mutuwo Koperani




Numeri 9:15
21 Mawu Ofanana  

Munawatsogoleranso usana ndi mtambo woti njo, ndi moto tolo usiku, kuwaunikira m'njira akayendamo.


koma Inu mwa nsoni zanu zazikulu simunawasiye m'chipululu; mtambo woti njo sunawachokere usana kuwatsogolera m'njira, ngakhale moto wa tolo usiku kuwaunikira panjira anayenera kuyendamo.


Anayala mtambo uwaphimbe; ndi moto uunikire usiku.


Ndipo msana anawatsogolera ndi mtambo ndi usiku wonse ndi kuunika kwa moto.


Ndipo Yehova anawatsogolera usana ndi mtambo njo kuwatsogolera m'njira; ndi usiku ndi moto njo, wakuwawalitsira; kuti ayende usana ndi usiku;


sanachotse mtambo usana, kapena mtambo wamoto usiku, pamaso pa anthu.


Ndipo kunali, ulonda wa mamawa, Yehova ali m'moto ndi m'mtambo njo anapenyera pa ulendo wa Aejipito, nauvuta ulendo wa Aejipito.


Tsiku loyamba la mwezi woyamba ukautse Kachisi wa chihema chokomanako.


Pamenepo mtambo unaphimba chihema chokomanako, ndi ulemerero wa Yehova unadzaza Kachisiyo.


Ndipo Mose sanathe kulowa m'chihema chokomanako, popeza mtambo unakhalabe pamenepo; ndi ulemerero wa Yehova unadzaza Kachisi.


Pakuti mtambo wa Yehova unakhala pa chihema msana, ndi usiku munali moto m'menemo, pamaso pa mbumba yonse ya Israele, m'maulendo ao onse.


Ndipo Yehova adzalenga pokhala ponse paphiri la Ziyoni, ndi pa misonkhano yake, mtambo ndi utsi usana, ndi kung'azimira kwa malawi a moto usiku; chifukwa kuti pa ulemerero wonse padzayalidwa chophimba.


Ndipo mtambo wa Yehova unali pamwamba pao msana, pakuyenda iwo kuchokera kuchigono.


ndipo adzawauza okhala m'dziko muno; adamva kuti inu Yehova muli pakati pa anthu awa; pakuti muoneka mopenyana, Yehova ndi mtambo wanu umaima pamwamba pao, ndipo muwatsogolera, ndi mtambo njo msana, ndi moto njo usiku.


Ndipo Mose anaika ndodozo pamaso pa Yehova m'chihema cha mboni.


Pakuti sindifuna, kuti mukhale osadziwa, abale, kuti makolo athu onse anali pansi pa mtambo, naoloka nyanja onse;


amene anakutsogolerani m'njira, kukufunirani malo akumanga mahema anu ndi moto usiku, kukuonetserani njira yoyendamo inu, ndi mumtambo usana.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa