Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Numeri 9:14 - Buku Lopatulika

14 Ndipo mlendo akakhala mwa inu, nakachitira Yehova Paska, azichita monga mwa lemba la Paska, ndi monga mwa chiweruzo chake; lemba likhale limodzi kwa inu, ndi kwa mlendo, ndi kwa wobadwa m'dziko.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

14 Ndipo mlendo akakhala mwa inu, nakachitira Yehova Paska, azichita monga mwa lemba la Paska, ndi monga mwa chiweruzo chake; lemba likhale limodzi kwa inu, ndi kwa mlendo, ndi kwa wobadwa m'dziko.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

14 Mlendo akakhala pakati panu, nafuna kuchita nao Paska ya Chauta, nayenso achite Paskayo potsata malamulo ake ndi malangizo ake. Kaya ndinu alendo kapena ndinu mbadwa, nonse mukhale ndi lamulo limodzi lokha.”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

14 “ ‘Mlendo amene akukhala pakati panu, nafuna kuchita nawo Paska ya Yehova, achite nawo motsata malamulo ndi malangizo ake. Muzikhala ndi malangizo ofanana a Paska; mbadwa kapena mlendo.’ ”

Onani mutuwo Koperani




Numeri 9:14
14 Mawu Ofanana  

Ndipo ana a Israele obwera kundende, ndi yense wakudzipatulira kuchokera chonyansa cha amitundu, kutsata iwowa, kufuna Yehova Mulungu wa Israele, anadza,


Ndipo Yehova anati kwa Mose ndi Aroni, Lemba la Paska ndi ili: mwana wa mlendo aliyense asadyeko;


Gulu lonse la Israele lizichita ichi.


Usamakunkha khunkha la m'munda wako wampesa, usamazitola zidagwazi za m'munda wako wampesa; uzisiyire wosauka ndi mlendo; Ine ndine Yehova Mulungu wanu.


Ndipo musamazilandira izi ku dzanja la mlendo ndi kubwera nazo zikhale chakudya cha Mulungu wanu; popeza zili nako kuvunda kwao; zili ndi chilema; sizidzalandirikira inu.


Chiweruzo chanu chifanefane ndi mlendo ndi wobadwa m'dziko; pakuti Ine ndine Yehova Mulungu wanu.


monga mwa kuwerenga kwake kwa zaka, chitapita choliza lipenga, uzigula kwa mnansi wako, ndi monga mwa kuwerenga kwa zaka za zipatso azigulitsa.


Kunena za khamu, pakhale lemba limodzi kwa inu, ndi kwa mlendo wakukhala kwanu, ndilo lemba losatha mwa mibadwo yanu; monga mukhala inu, momwemo mlendo pamaso pa Yehova.


Pakhale chilamulo chimodzi ndi chiweruzo chimodzi kwa inu ndi kwa mlendo wakukhala kwanu.


makanda anu, akazi anu, ndi mlendo wanu wakukhala pakati pa zigono zanu, kuyambira wotema nkhuni kufikira wotunga madzi;


Sonkhanitsani anthu, amuna ndi akazi ndi ana aang'ono, ndi mlendo wokhala m'midzi mwanu, kuti amve, ndi kuti aphunzire kuopa Yehova Mulungu wanu, ndi kusamalira kuchita mau onse a chilamulo ichi;


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa