Baibulo la pa intaneti

Zotsatsa


Baibulo lonse Chipangano Chakale Chipangano Chatsopano




Eksodo 26:30 - Buku Lopatulika

Ndipo uutse chihema monga mwa makhalidwe ake amene anakusonyeza m'phiri.

Onani mutuwo

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

Ndipo uutse Kachisi monga mwa makhalidwe ake amene anakusonyeza m'phiri.

Onani mutuwo

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Motero upange chihema changa monga momwe ndikukulangizira paphiri pano.

Onani mutuwo

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

“Upange chihema mofanana ndi momwe ndinakuonetsera pa phiri paja.

Onani mutuwo



Eksodo 26:30
14 Mawu Ofanana  

Chonsechi, anati Davide, anandidziwitsa ndi kuchilemba kuchokera kwa dzanja la Yehova; ndizo ntchito zonse za chifaniziro ichi.


Ndipo uyang'anire uzipanga monga mwachifaniziro chao, chimene anakuonetsa m'phirimo.


Monga mwa zonse Ine ndilikuonetsa iwe, chifaniziro cha chihema, ndi chifaniziro cha zipangizo zake zonse, momwemo uchimange.


Ndipo uzikuta matabwa ndi golide, ndi kupanga mphete zao zagolide zopisamo mitandayo; uzikutanso mitandayo ndi golide.


Ulipange lagweregwere ndi matabwa; monga anakuonetsa m'phirimo; alipange momwemo.


Tsiku loyamba la mwezi woyamba ukautse Kachisi wa chihema chokomanako.


Pamenepo Akohati anayenda, ndi kunyamula zopatulika, ndi enawo anautsiratu chihema asanafike iwowa.


Ndipo mapangidwe ake a choikaponyali ndiwo golide wosula; kuyambira tsinde lake kufikira maluwa ake anachisula; monga mwa maonekedwe ake Yehova anaonetsa Mose, momwemo anachipanga choikaponyali.


Chihema cha umboni chinali ndi makolo athu m'chipululu, monga adalamula Iye wakulankhula ndi Mose, achipange ichi monga mwa chithunzicho adachiona.


Mtumiki wa malo opatulika, ndi wa chihema choona, chimene Ambuye anachimanga, si munthu ai.


amene atumikira chifaniziro ndi mthunzi wa zakumwambazo monga Mose achenjezedwa m'mene anafuna kupanga chihema: pakuti, Chenjera, ati, uchite zonse monga mwa chitsanzocho chaonetsedwa kwa iwe m'phiri.


Pomwepo padafunika kuti zifaniziro za zinthu za mu Mwamba ziyeretsedwe ndi izi; koma zam'mwamba zenizeni ziyeretsedwe ndi nsembe zoposa izi.


Ndipo msonkhano wonse wa ana a Israele unasonkhana ku Silo, nuutsa komweko chihema chokomanako; ndipo dziko linawagonjera.