Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Eksodo 27:8 - Buku Lopatulika

8 Ulipange lagweregwere ndi matabwa; monga anakuonetsa m'phirimo; alipange momwemo.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

8 Ulipange lagweregwere ndi matabwa; monga anakuonetsa m'phirimo; alipange momwemo.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

8 Ndipo guwalo udzalipange mogoba m'kati mwake. Ulipange monga momwe ndikukulangizira paphiri pano.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

8 Guwalo likhale lamatabwa ndi logoba mʼkati mwake. Ulipange monga momwe ndinakuonetsera pa phiri paja.

Onani mutuwo Koperani




Eksodo 27:8
9 Mawu Ofanana  

Pamenepo Davide anapatsa Solomoni mwana wake chifaniziro cha chipinda cholowera cha Kachisi, ndi cha nyumba zake, ndi cha zosungiramo chuma zake, ndi cha zipinda zosanjikizana zake, ndi cha zipinda zake za m'katimo, ndi cha Kachisi wotetezerepo;


Chonsechi, anati Davide, anandidziwitsa ndi kuchilemba kuchokera kwa dzanja la Yehova; ndizo ntchito zonse za chifaniziro ichi.


Ndipo uyang'anire uzipanga monga mwachifaniziro chao, chimene anakuonetsa m'phirimo.


Monga mwa zonse Ine ndilikuonetsa iwe, chifaniziro cha chihema, ndi chifaniziro cha zipangizo zake zonse, momwemo uchimange.


Koma andilambira Ine kwachabe, ndi kuphunzitsa maphunzitso, malangizo a anthu.


Chihema cha umboni chinali ndi makolo athu m'chipululu, monga adalamula Iye wakulankhula ndi Mose, achipange ichi monga mwa chithunzicho adachiona.


amene atumikira chifaniziro ndi mthunzi wa zakumwambazo monga Mose achenjezedwa m'mene anafuna kupanga chihema: pakuti, Chenjera, ati, uchite zonse monga mwa chitsanzocho chaonetsedwa kwa iwe m'phiri.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa