Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Eksodo 27:9 - Buku Lopatulika

9 Upangenso bwalo la chihema; pa mbali yake ya kumwera, kumwera, pakhale nsalu zotchingira za kubwalo za nsalu yabafuta wa thonje losansitsa, utali wake wa pa mbali imodzi mikono zana;

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

9 Upangenso bwalo la chihema; pa mbali yake ya kumwera, kumwera, pakhale nsalu zochingira za kubwalo za nsalu yabafuta wa thonje losansitsa, utali wake wa pa mbali imodzi mikono zana;

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

9 “Pambuyo pake upange bwalo la chihema, lochingidwa. Chakumwera kwake kukhale nsalu zochinga za bafuta wosalala ndi wopikidwa bwino, kutalika kwa mbali imodzi kukhale mamita 46.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

9 “Upange bwalo la chihema. Mbali yakummwera ikhale yotalika mamita 46 ndipo ikhale ndi nsalu yotchinga yofewa yosalala yolukidwa bwino.

Onani mutuwo Koperani




Eksodo 27:9
29 Mawu Ofanana  

Ndipo bwalo la m'kati analimanga mizere itatu ya miyala yosemasema, ndi mzere umodzi wa mitanda yamkungudza.


Tsiku lomwelo mfumu inapatulira Mulungu pakati pake pa bwalo la ku khomo la nyumba ya Yehova; pakuti pomwepo anapereka nsembe yopsereza ndi nsembe yaufa, ndi mafuta a nsembe zamtendere; popeza guwa la nsembe lamkuwa linali pamaso pa Yehova lidachepa kulandira nsembe zopsereza, ndi nsembe zaufa, ndi mafuta a nsembe zamtendere.


Namangiranso khamu lonse la kuthambo maguwa a nsembe m'mabwalo awiri a nyumba ya Yehova.


Anamanganso bwalo la ansembe, ndi bwalo lalikulu, ndi zitseko za kubwalo, nakuta zitseko zake ndi mkuwa.


Lowani kuzipata zake ndi chiyamiko, ndi kumabwalo ake ndi chilemekezo: Myamikeni; lilemekezeni dzina lake.


M'mabwalo a nyumba ya Yehova, pakati pa inu, Yerusalemu. Aleluya.


Pakuti tsiku limodzi m'mabwalo anu likoma koposa masiku ambirimbiri akukhala pena. Kukhala ine wapakhomo m'nyumba ya Mulungu wanga, kundikonda ine koposa kugonera m'mahema a choipa.


Iwo ookedwa m'nyumba ya Yehova, adzaphuka m'mabwalo a Mulungu wathu.


ndi nsichi zake makumi awiri, ndi makamwa ao makumi awiri akhale amkuwa; zokowera za nsichi ndi mitanda yake zikhale zasiliva.


nsalu zotchingira za kubwalo, nsichi zake, ndi makamwa ake, ndi nsalu yotsekera ku chipata cha pabwalo;


Ndipo anapanga magango makumi asanu m'mphepete mwa nsalu imodzi, ya kuthungo, ya chilumikizano, naika magango makumi asanu m'mphepete mwa nsalu ya kuthungo, ya chilumikizano china.


nsalu zotchingira za pabwalo, nsichi zake, ndi makamwa ake, ndi nsalu yotsekera pa chipata cha pabwalo, zingwe zake, ndi zichiri zake, ndi zipangizo zonse za ntchito ya Kachisi, za ku chihema chokomanako;


Ndipo anautsa mpanda pozungulira pa chihema ndi guwa la nsembe, napachika nsalu yotsekera pa chipata cha pabwalo. Momwemo Mose anatsiriza ntchitoyi.


Ndipo ukamange mpandawo pozungulira, ndi kupachika nsalu yotsekera pa chipata cha pabwalo.


Anamanganso nsanamira za mikono makumi asanu ndi limodzi; ndi bwalo la pakati pa chipata lidafikira kunsanamira.


Pamenepo analowa nane kubwalo lakunja, ndipo taonani, panali zipinda, ndi moyalidwa miyala mokonzekera bwalo pozungulira ponse; moyalidwa miyalamo munali zipinda makumi atatu.


Ndi chipata cha bwalo lakunja choloza kumpoto anachiyesa m'litali mwake, ndi kupingasa kwake zonse mikono zana.


Ndipo panali chipata cha bwalo lam'kati, chopenyana ndi chipata chinzake chakunja kumpoto, ndi cha kum'mawa; ndipo anayesa kuyambira kuchipata kufikira kuchipata mikono zana.


Pamenepo analowa nane pa chipata cha kumwera m'bwalo lam'kati, nayesa chipata cha kumwera, monga mwa miyeso yomweyi;


Ndipo analowa ndine m'bwalo lam'kati kuloza kum'mawa, nayesa chipata cha kum'mawa monga mwa miyeso yomweyi;


Ndi kunja kwa chipata cha m'kati kunali tinyumba ta oimba m'bwalo lam'kati, kumbali ya chipata cha kumpoto; ndipo tinaloza kumwera, kena kumbali ya chipata cha kum'mawa kanaloza kumpoto.


Pandunji pa mikono makumi awiri a bwalo lam'kati, ndi pandunji pa moyalamo mwa miyala, mwa bwalo lakunja, panali khonde lam'mwamba, lokomana ndi khonde linzake losanjikika pachiwiri.


ndi nsalu zotchinga za kubwalo, ndi nsalu yotsekera pa chipata cha pabwalo, lokhala ku chihema, ndi ku guwa la nsembe pozungulira, ndi zingwe zake za ku ntchito zake zonse.


ndi nsalu zotchingira za pabwalo, ndi nsalu yotsekera ku chipata cha pabwalo lili pa chihema ndi paguwa la nsembe pozungulira, ndi zingwe zao, ndi zipangizo zonse za ntchito zao, ndi zonse achita nazo; m'menemo muli ntchito zao.


ndi nsichi za kubwalo kozungulira, ndi makamwa ake, ndi zichiri zake, ndi zingwe zake, pamodzi ndi zipangizo zake zonse, ndi ntchito yake yonse; ndipo muziwerenga zipangizo za udikiro wa akatundu ao ndi kuwatchula maina ao.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa