Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Yoswa 18:1 - Buku Lopatulika

1 Ndipo msonkhano wonse wa ana a Israele unasonkhana ku Silo, nuutsa komweko chihema chokomanako; ndipo dziko linawagonjera.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

1 Ndipo msonkhano wonse wa ana a Israele unasonkhana ku Silo, nuutsa komweko chihema chokomanako; ndipo dziko linawagonjera.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

1 Ataligonjetsa dziko lonselo, Aisraele onse adasonkhana ku Silo, ndipo adamangako chihema chamsonkhano.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

1 Atagonjetsa dziko lonse Aisraeli anasonkhana ku Silo ndipo anayimikako tenti ya msonkhano.

Onani mutuwo Koperani




Yoswa 18:1
26 Mawu Ofanana  

Pakuti sindinakhale m'nyumba kuyambira tsiku lija ndinatulutsa ana a Israele ku Ejipito kufikira lero lomwe, koma ndinayenda m'chihema ndi m'nyumba wamba.


Ndipo Yerobowamu ananena ndi mkazi wake, Unyamuke, nudzizimbaitse, ungadziwike kuti ndiwe mkazi wa Yerobowamu, nupite ku Silo; taona, kumeneko kuli Ahiya mneneri uja anandiuza ine ndidzakhala mfumu ya anthu awa.


Natero mkazi wa Yerobowamu, nanyamuka nanka ku Silo, nalowa m'nyumba ya Ahiya. Koma Ahiya sanathe kupenya, popeza maso ake anali tong'o, chifukwa cha ukalamba wake.


Motero Solomoni anachotsa Abiyatara asakhalenso wansembe wa Yehova, kuti akakwaniritse mau a Yehova amene aja adalankhula ku Silo za mbumba ya Eli.


Nalowa anawo, nalandira dzikoli likhale laolao, ndipo munagonjetsa pamaso pao okhala m'dziko, ndiwo Akanani, ndi kuwapereka m'dzanja mwao, pamodzi ndi mafumu ao, ndi mitundu ya anthu ya m'dziko, kuti achite nao chifuniro chao.


ndipo anachokera chokhalamo cha ku Silo, chihemacho adachimanga mwa anthu;


Ndipo anapanda otsutsana naye kumbuyo; nawapereka akhale otonzeka kosatha.


pamenepo ndidzayesa nyumba iyi ifanane ndi Silo, ndipo ndidzayesa mzinda uwu chitemberero cha kwa mitundu yonse ya dziko lapansi.


Bwanji mwanenera m'dzina la Yehova, kuti, Nyumba iyi idzafanana ndi Silo, mzinda uwu udzakhala bwinja lopanda wokhalamo? Ndipo anthu onse anamsonkhanira Yeremiya m'nyumba ya Yehova.


anadza anthu ochokera ku Sekemu, ndi ku Silo, ndi ku Samariya, anthu makumi asanu ndi atatu, atameta ndevu zao, atang'amba zovala zao, atadzitematema, anatenga nsembe zaufa ndi lubani m'manja mwao, kunka nazo kunyumba ya Yehova.


ndi dziko lagonjera Yehova; mutatero mudzabwerere, ndi kukhala osachimwira Yehova ndi Israele; ndipo dziko ili lidzakhala lanulanu pamaso pa Yehova.


Chimenenso makolo athu akudza m'mbuyo, analowa nacho ndi Yoswa polandira iwo zao za amitundu, amene Mulungu anawaingitsa pamaso pa makolo athu, kufikira masiku a Davide;


Ndipo anatsala mwa ana a Israele mafuko asanu ndi awiri osawagawira cholowa chao.


Ndipo amunawo ananyamuka, namuka; ndipo Yoswa analamulira opita kulemba dzikowo, ndi kuti, Mukani, muyendeyende pakati padziko, ndi kulilemba, nimubwerenso kwa ine, ndipo ndidzakuloterani maere pano pamaso pa Yehova pa Silo.


Izi ndizo zolowa anazigawa Eleazara wansembe, ndi Yoswa mwana wa Nuni, ndi akulu a nyumba za atate a mafuko a ana a Israele, zikhale zaozao, ndi kulota maere ku Silo pamaso pa Yehova ku khomo la chihema chokomanako. Momwemo anatha kuligawa dziko.


nanena nao ku Silo m'dziko la Kanani, ndi kuti Yehova analamulira mwa dzanja la Mose kuti atipatse mizinda yokhalamo ife, ndi mabusa a zoweta zathu.


Pamene ana a Israele anamva ichi msonkhano wonse wa ana a Israele anasonkhana ku Silo, kuti awakwerere kuwathira nkhondo.


Koma mukayesa dziko la cholowa chanu nchodetsa, olokani kulowa m'dziko la cholowa cha Yehova m'mene chihema cha Yehova chikhalamo, nimukhale nacho cholowa pakati pa ife; koma musapikisana ndi Yehova kapena kupikisana nafe, ndi kudzimangira nokha guwa la nsembe, pamodzi ndi guwa la nsembe la Yehova Mulungu wathu.


Ndipo ana a Rubeni, ndi ana a Gadi, ndi hafu la fuko la Manase anabwerera, nachoka kwa ana a Israele ku Silo, ndiwo wa m'dziko la Kanani kunka ku dziko la Giliyadi, ku dziko laolao, limene anakhala eni ake, monga mwa lamulo la Yehova, mwa dzanja la Mose.


Motero anadziikira fano losema la Mika, limene adalipanga, masiku onse okhala nyumba ya Mulungu ku Silo.


Ndipo anapeza mwa anthu a Yabesi-Giliyadi anamwali mazana anai osadziwa mwamuna mogona naye; nabwera nao kumisasa ku Silo, ndiwo a m'dziko la Kanani.


Nati iwo, Taonani, pali madyerero a Yehova chaka ndi chaka ku Silo, ndiko kumpoto kwa Betele, kum'mawa kwa mseu wokwera kuchokera ku Betele kunka ku Sekemu, ndi kumwera kwa Lebona.


Ndipo atamletsa kuyamwa anakwera naye, pamodzi ndi ng'ombe ya zaka zitatu, ndi efa wa ufa, ndi thumba la vinyo, nafika naye kunyumba ya Yehova ku Silo; koma mwanayo anali wamng'ono.


Ndipo munthuyo akakwera chaka ndi chaka kutuluka m'mzinda mwake kukalambira ndi kupereka nsembe kwa Yehova wa makamu mu Silo. Ndipo pomwepo panali ana aamuna awiri a Eli, ansembe a Yehova, ndiwo Hofeni ndi Finehasi.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa