Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Ahebri 9:23 - Buku Lopatulika

23 Pomwepo padafunika kuti zifaniziro za zinthu za mu Mwamba ziyeretsedwe ndi izi; koma zam'mwamba zenizeni ziyeretsedwe ndi nsembe zoposa izi.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

23 Pomwepo padafunika kuti zifaniziro za zinthu za m'Mwamba ziyeretsedwe ndi izi; koma zam'mwamba zenizeni ziyeretsedwe ndi nsembe zoposa izi.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

23 Tsono padaafunika kuti zinthu zongofanizira zenizeni za Kumwamba, ziyeretsedwe ndi miyambo imeneyi. Koma kuti za Kumwamba zenizenizo ziyeretsedwe, padaafunika nsembe zina zoposa zimenezo.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

23 Tsono panafunika kuti zinthu zingofanizira zenizeni za kumwamba, ziyeretsedwe ndi nsembe zimenezi, koma zinthu za kumwamba zenizenizo kuti ziyeretsedwe panafunika nsembe zina zoposa zimenezo.

Onani mutuwo Koperani




Ahebri 9:23
14 Mawu Ofanana  

Kodi sanayenere Khristu kumva zowawa izi, ndi kulowa ulemerero wake?


ndipo anati kwa iwo, Kotero kwalembedwa, kuti Khristu amve zowawa, nauke kwa akufa tsiku lachitatu;


Ndipo ngati ndipita kukakonzera inu malo, ndidzabweranso, ndipo ndidzalandira inu kwa Ine ndekha; kuti kumene kuli Ineko, mukakhale inunso.


Potero tsopano inu ndi bwalo la akulu a milandu muzindikiritse kapitao wamkulu kuti atsike naye kwa inu, monga ngati mufuna kudziwitsitsa bwino za iye; koma tadzikonzeratu timuphe asanayandikire iye.


ndizo mthunzi wa zilinkudzazo; koma thupi ndi la Khristu.


Pakuti chilamulo, pokhala nao mthunzi wa zokoma zilinkudza, osati chifaniziro chenicheni cha zinthuzo, sichikhozatu, ndi nsembe zomwezi chaka ndi chaka, zimene azipereka kosalekeza, kuwayesera angwiro iwo akuyandikira.


Pakuti sikutheka kuti mwazi wa ng'ombe zamphongo, ndi mbuzi ukachotsera machimo.


amene atumikira chifaniziro ndi mthunzi wa zakumwambazo monga Mose achenjezedwa m'mene anafuna kupanga chihema: pakuti, Chenjera, ati, uchite zonse monga mwa chitsanzocho chaonetsedwa kwa iwe m'phiri.


koposa kotani nanga mwazi wa Khristu amene anadzipereka yekha wopanda chilema kwa Mulungu mwa Mzimu wosatha, udzayeretsa chikumbumtima chanu kuchisiyanitsa ndi ntchito zakufa, kukatumikira Mulungu wamoyo?


Pakuti Khristu sanalowe m'malo opatulika omangika ndi manja, akutsanza oonawo; komatu mu Mwamba momwe, kuonekera tsopano pamaso pa Mulungu chifukwa cha ife;


Ndipo aimba nyimbo yatsopano, ndi kunena, Muyenera kulandira bukulo, ndi kumasula zizindikiro zake; chifukwa mwaphedwa, ndipo mwagulira Mulungu ndi mwazi wanu anthu a mafuko onse, ndi manenedwe onse, ndi mitundu yonse,


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa