Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Numeri 10:21 - Buku Lopatulika

21 Pamenepo Akohati anayenda, ndi kunyamula zopatulika, ndi enawo anautsiratu chihema asanafike iwowa.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

21 Pamenepo Akohati anayenda, ndi kunyamula zopatulika, ndi enawo anautsiratu Kachisi asanafike iwowa.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

21 Tsono Akohati atasenza zinthu zopatulika, adanyamuka. Malo opatulika anali atamangidwiratu iwowo asanafike.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

21 Kenaka Akohati ananyamuka atanyamula zinthu zopatulika. Chihema chinkayenera kuyimikidwa iwo asanafike.

Onani mutuwo Koperani




Numeri 10:21
11 Mawu Ofanana  

Pamenepo Davide anati, Sayenera ena kusenza likasa la Mulungu koma Alevi ndiwo; pakuti Yehova anawasankha iwo kusenza likasa la Mulungu, ndi kumtumikira Iye kosatha.


Awa ndi ana a Levi monga mwa nyumba za makolo ao, ndiwo akulu a nyumba za makolo a iwo owerengedwa mwa chiwerengero cha maina mmodzimmodzi, akugwira ntchito ya utumiki wa nyumba ya Yehova, kuyambira a zaka makumi awiri ndi mphambu.


Ndipo akati amuke nacho chihemacho, Alevi amgwetse, ndipo akati achimange, Alevi achiimike; ndipo mlendo akayandikizako amuphe.


Ndipo anagwetsa chihema; ndi ana a Geresoni, ndi ana a Merari, akunyamula chihema, anamuka nacho.


Ndi pa gulu la fuko la ana a Gadi anayang'anira Eliyasafu mwana wa Deuwele.


Pamenepo khamu la Alevi azimuka nacho chihema chokomanako, pakati pa makamu; monga amamanga mahema ao, momwemo azimuka ulendo wao, munthu yense pamalo pake, monga mwa mbendera zao.


Koma asalowe kukaona zopatulikazo pozikulunga, kuti angafe.


Koma sanapatse ana a Kohati kanthu; popeza ntchito yao ndiyo ya zinthu zopatulika, zimene amazisenza pa mapewa ao.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa