Ahebri 8:5 - Buku Lopatulika5 amene atumikira chifaniziro ndi mthunzi wa zakumwambazo monga Mose achenjezedwa m'mene anafuna kupanga chihema: pakuti, Chenjera, ati, uchite zonse monga mwa chitsanzocho chaonetsedwa kwa iwe m'phiri. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 20145 amene atumikira chifaniziro ndi mthunzi wa zakumwambazo monga Mose achenjezedwa m'mene anafuna kupanga chihema: pakuti, Chenjera, ati, uchite zonse monga mwa chitsanzocho chaonetsedwa kwa iwe m'phiri. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa5 Ntchito za chipembedzo zimene iwo amachita, zili ngati chithunzi chongofanizira zenizeni za Kumwamba. Paja zidaateronso ndi Mose: pamene iye adaati amange chihema, Mulungu adaamlangiza kuti, “Upangetu zonse molingana ndi chitsanzo chimene ndidaakuwonetsa paphiri paja.” Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero5 Iwo amatumikira pamalo opatulika amene ndi chithunzi ndi chifanizo cha zimene zili kumwamba. Ichi ndi chifukwa chake Mose anachenjezedwa pamene anali pafupi kumanga Tenti: “Uwonetsetse kuti wapanga zonse monga momwe ndikukuonetsera pa phiri pano.” Onani mutuwo |