Ndipo Yakobo anatcha dzina la malo amenewo, Penuwele: chifukwa ndaonana ndi Mulungu nkhope ndi nkhope, ndipo wapulumuka moyo wanga.
Eksodo 24:10 - Buku Lopatulika ndipo anapenya Mulungu wa Israele; ndipo pansi pa mapazi ake panali ngati mayalidwe oyera a miyala yasafiro, ndi ngati thupi la thambo loti mbee. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 ndipo anapenya Mulungu wa Israele; ndipo pansi pa mapazi ake panali ngati mayalidwe oyera a miyala yasafiri, ndi ngati thupi la thambo loti mbee. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa ndipo adaonana ndi Mulungu wa Aisraele. Pansi pa mapazi ake panali china chooneka ngati mseu wopangidwa ndi mwala wa safiro woyalidwa bwino, wa maonekedwe onga thambo. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero ndipo anaona Mulungu wa Israeli. Pansi pa mapazi ake panali njira yoyendamo yopangidwa ndi mwala wa safiro woyalidwa bwino wa maonekedwe owala ngati thambo. |
Ndipo Yakobo anatcha dzina la malo amenewo, Penuwele: chifukwa ndaonana ndi Mulungu nkhope ndi nkhope, ndipo wapulumuka moyo wanga.
Ndipo kudamchera iye pamene anaoloka pa Penuwele, ndipo iye anatsimphina ndi ntchafu yake.
Ndipo anati, Chifukwa chake tamverani mau a Yehova, Ndinaona Yehova alikukhala pa mpando wake wachifumu, ndi khamu lonse lakumwamba lili chilili m'mbali mwake, ku dzanja lamanja ndi lamanzere.
Ndipo tsopano, Yehova Mulungu wa Israele, achitike mau anu amene munanena kwa Davide mtumiki wanu.
Koma sanatulutse dzanja lake pa akulu a ena a Israele; ndipo anapenya Mulungu, nadya, namwa.
Ananenanso, Ine ndine Mulungu wa atate wako, Mulungu wa Abrahamu, Mulungu wa Isaki, ndi Mulungu wa Yakobo. Ndipo Mose anabisa nkhope yake; popeza anaopa kuyang'ana Mulungu.
Ananenanso, Sungathe kuona nkhope yanga; pakuti palibe munthu adzandiona Ine ndi kukhala ndi moyo.
ndipo pamene ndichotsa dzanja langa udzaona m'mbuyo mwanga; koma nkhope yanga siidzaoneka.
Manja ake akunga zing'anda zagolide zoikamo zonyezimira zoti biriwiri. Thupi lake likunga chopanga cha minyanga cholemberapo masafiro.
Nati, Ndaniyo atuluka ngati mbandakucha, wokongola ngati mwezi, woyera ngati dzuwa, woopsa ngati nkhondo ndi mbendera?
Omveka ake anakonzeka koposa chipale chofewa, nayera koposa mkaka, matupi ao anafiira koposa timiyala toti psu; maonekedwe ao ananga a safiro wa mtengo wapatali.
Ndipo kunali chaka cha makumi atatu, mwezi wachinai, tsiku lachisanu la mwezi, pokhala ine pakati pa andende kumtsinje Kebara, kunatseguka kumwamba, ndipo ndinaona masomphenya a Mulungu.
Ndipo ndinapenya, ndipo taonani, kuthambo lokhala pamwamba pa mitu ya akerubi kudaoneka ngati mwala wasafiro, ngati maonekedwe a chifaniziro cha mpando wachifumu pamwamba pao.
Pakuti mnyamata wa mbuye wanga inu akhoza bwanji kulankhula ndi mbuye wanga inu? Pakuti ine tsopano apa mulibenso mphamvu mwa ine, osanditsaliranso mpweya.
Ndimanena naye pakamwa ndi pakamwa, moonekera, osati mophiphiritsa; ndipo amapenyerera maonekedwe a Yehova; potero munalekeranji kuopa kutsutsana naye mtumiki wanga, Mose.
ndipo Iye anasandulika pamaso pao; ndipo nkhope yake inawala monga dzuwa, ndi zovala zake zinakhala zoyera mbuu monga kuwala.
Kulibe munthu anaona Mulungu nthawi zonse; Mwana wobadwa yekha wakukhala pa chifuwa cha Atate, Iyeyu anafotokozera.
Yesu ananena naye, Kodi ndili ndi inu nthawi yaikulu yotere, ndipo sunandizindikire, Filipo? Iye amene wandiona Ine waona Atate; unena iwe bwanji, Mutionetsere Atate?
Sikuti munthu wina waona Atate, koma Iye amene ali wochokera kwa Mulungu, ameneyo waona Atate.
amene Iye yekha ali nao moyo wosatha, wakukhala m'kuunika kosakhozeka kufikako; amene munthu sanamuone, kapena sangathe kumuona; kwa Iye kukhale ulemu ndi mphamvu yosatha. Amen.
Palibe munthu adamuona Mulungu nthawi iliyonse; tikakondana wina ndi mnzake, Mulungu akhala mwa ife, ndi chikondi chake chikhala changwiro mwa ife;
Ndipo m'dzanja lake lamanja munali nyenyezi zisanu ndi ziwiri; ndi m'kamwa mwake mudatuluka lupanga lakuthwa konsekonse; ndipo nkhope yake ngati dzuwa lowala mu mphamvu yake.
ndipo unakhala nao ulemerero wa Mulungu; kuunika kwake kunafanana ndi mwala wa mtengo wake woposa, ngati mwala wayaspi, wonyezimira, ngati krustalo;
ndipo maonekedwe a Iye wokhalapo anafanana ndi mwala wa jaspi, ndi sardiyo; ndipo panali utawaleza wozinga mpando wachifumu, maonekedwe ake ngati smaragido.