Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Maliro 4:7 - Buku Lopatulika

7 Omveka ake anakonzeka koposa chipale chofewa, nayera koposa mkaka, matupi ao anafiira koposa timiyala toti psu; maonekedwe ao ananga a safiro wa mtengo wapatali.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

7 Omveka ake anakonzeka koposa chipale chofewa, nayera koposa mkaka, matupi ao anafiira koposa timiyala toti psu; maonekedwe ao ananga a safiro wa mtengo wapatali.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

7 Akalonga ake anali oŵala koposa chisanu chambee, oyera kuposa mkaka. Matupi ao anali ofiira kupambana miyala ya rubi. Anali ndi maonekedwe okongola ngati miyala ya safiro.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

7 Akalonga ake anali owala koposa chisanu chowundana ndi oyera kuposa mkaka. Matupi awo anali ofiira kuposa miyala ya rubi, maonekedwe awo ngati miyala ya safiro.

Onani mutuwo Koperani




Maliro 4:7
15 Mawu Ofanana  

Sailinganiza ndi golide wa Ofiri, ndi sohamu wa mtengo wake wapatali kapena safiro.


Korali kapena ngale sizikumbukikapo. Mtengo wake wa nzeru uposa wa korali wofiira.


Kuti ana athu aamuna akhale ngati mmera udakula usanakhwime; ana athu aakazi ngati nsanamira za kungodya, zosema zikometsere nyumba ya mfumu.


Mundiyeretse ndi hisope ndipo ndidzayera; munditsuke ndipo ndidzakhala wa mbuu woposa matalala.


ndipo anapenya Mulungu wa Israele; ndipo pansi pa mapazi ake panali ngati mayalidwe oyera a miyala yasafiro, ndi ngati thupi la thambo loti mbee.


Wokondedwa wanga ali woyera ndi wofiira, womveka mwa zikwi khumi.


Miyendo yake ikunga zoimiritsa za mwala wonyezimira, zogwirika m'kamwa mwa golide: Maonekedwe ake akunga Lebanoni, okometsetsa ngati mikungudza.


Atatha masiku khumiwo tsono, anaona kuti maonekedwe ao ndi kunenepa kwao anaposa anyamata onse adadyawo zakudya za mfumu.


Pakuti iye adzakhala wamkulu pamaso pa Ambuye, ndipo sadzamwa konse vinyo kapena kachasu; nadzadzazidwa ndi Mzimu Woyera, kuyambira asanabadwe.


pakuti taona, udzaima, nudzabala mwana wamwamuna; pamutu pake sipadzafika lumo; pakuti mwanayo adzakhalira kwa Mulungu Mnaziri chibadwire; nadzayamba iye kupulumutsa Israele m'dzanja la Afilisti.


koma anati kwa ine, Taona, udzaima, ndi kubala mwana wamwamuna; ndipo tsopano usamwe vinyo kapena choledzeretsa, nusadye chilichonse chodetsa; pakuti mwanayo adzakhalira kwa Mulungu Mnaziri chibadwire mpaka tsiku la kufa kwake.


Pomwepo anamfotokozera mtima wake wonse, nanena naye, Pamutu panga sipanapite lumo, pakuti ndine Mnaziri wa Mulungu chiyambire mimba ya mai wanga; akandimeta, mphamvu yanga idzandichokera, ndidzakhala wofooka wakunga munthu wina aliyense.


Ndipo anatumiza munthu, nabwera naye. Tsono iye anali wofiirira, ndi wa nkhope yokongola, ndi maonekedwe okoma. Ndipo Yehova anati, Nyamuka umdzoze, pakuti ndi ameneyu.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa